LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w17 January masa. 12-16
  • Muziyamikila Mphatso Yanu ya Ufulu Wosankha Zocita

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muziyamikila Mphatso Yanu ya Ufulu Wosankha Zocita
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • TINGAPHUNZILENJI KWA YEHOVA NA YESU?
  • KUKWANITSA KAPENA KULEPHELA KUSEŴENZETSA BWINO UFULUWO
  • PEWANI KUSEŴENZETSA UFULU WANU MOLAKWA
  • TIZILEMEKEZA UFULU WA ENA
  • Njila Yopezela Ufulu Weni-weni
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Tumikilani Yehova, Mulungu wa Ufulu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
w17 January masa. 12-16
Abulahamu, Sara, ndi ena acoka ku Uri

Muziyamikila Mphatso Yanu ya Ufulu Wosankha Zocita

“Pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.”—2 AKOR. 3:17.

NYIMBO: 62, 65

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi ni mphatso iti yapadela imene Mulungu anatipatsa?

  • Kodi ufulu wathu wocita zinthu ungaonetse bwanji ngati timam’kondadi Yehova?

  • Nanga tingalemekeze bwanji ufulu wa ena pa zimene amasankha?

1, 2. (a) Kodi anthu ali na maganizo osiyana-siyana ati pa nkhani ya ufulu wosankha zocita? (b) Nanga Baibo imatiphunzitsa ciani za ufulu umenewo? Ndipo tikambilana mafunso ati?

MZIMAYI wina anafunikila kusankha zocita pa nkhani inayake. Ndiye anapempha mnzake kuti: “Usayambe zonifunsa kuti nanga iwe uganiza ciani, ungoniuza cabe zocita. Sinifuna zovutika n’kuganiza-ganiza.” Mzimayiyu anasankha kungouzidwa zocita, m’malo moseŵenzetsa mphatso yabwino kwambili imene Mlengi wake anam’patsa. Inde, mphatso ya ufulu wosankha wekha zocita. Nanga bwanji imwe? Kodi mumakonda kusankha mwekha zocita? Kapena mumafuna anthu ena kukusankhilani? Mumaiona bwanji nkhani ya ufulu wocita zinthu?

2 Anthu akhala akutsutsana kwa zaka zambili pa nkhani imeneyi. Ena amati kulibe ufulu wosankha zocita. Mulungu anaikilatu zonse zimene timacita. Ena amati tingakhale na ufulu weniweni ngati tingaloledwe kumacita zilizonse zimene tingafune. Conco, kuti nkhaniyi tiimvetse bwino tifunika kupita ku Mau a Mulungu, Baibo. Cifukwa ciani? Cifukwa imaonetsa kuti Yehova anatilenga ndi ufulu wosankha zocita, kapena kuti nzelu za kuganiza ndi kusankha zocita. (Ŵelengani Yoswa 24:15.) Baibo imayankhanso mafunso monga akuti: Kodi ufulu wosankha zocita umenewu tiyenela kuuseŵenzetsa bwanji? Kodi uli na malile? Kodi ndi ufulu wathu umenewu, tingaonetse bwanji mlingo wa cikondi cathu kwa Yehova? Nanga tingalemekeze bwanji ufulu wa ena pa zosankha zawo?

TINGAPHUNZILENJI KWA YEHOVA NA YESU?

3. Kodi Yehova amapeleka citsanzo canji poseŵenzetsa ufulu wake?

3 Yehova yekha ndiye ali na ufulu wocita ciliconse cimene angafune, koma mmene amauseŵenzetsela amatipatsa citsanzo cabwino ngako. Mwacitsanzo, anasankha mtundu wa Aisiraeli kukhala anthu a dzina lake, ndi “cuma cake capadela.” (Deut. 7:6-8) Uku sikunali kungosankha cimene wakonda cabe ayi. Kunali kukwanilitsa lonjezo limene Yehova anapeleka kale-kale kwa bwenzi lake Abulahamu. (Gen. 22:15-18) Ndiponso, nthawi zonse Yehova amaseŵenzetsa ufulu wake mogwilizana ndi makhalidwe ake a cikondi na cilungamo. Timaona izi ndi mmene anali kupelekela cilango kwa Aisiraeli, amene anam’pandukila mobweleza-bweleza. Amati iwo akalapa moona mtima, anali kuwaonetsa cikondi ndi cifundo cake, pokamba kuti: “Ndidzathetsa kusakhulupilika kwawo. Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga.” (Hos. 14:4) Ha, n’citsanzo cabwino cotani nanga, coseŵenzetsa ufulu wake kupindulitsa ena!

4, 5. (a) Ndani anali woyamba kupatsidwako mphatso ya ufulu wosankha zocita? Nanga anaiseŵenzetsa bwanji? (b) Aliyense afunika kudzifunsa funso liti?

4 Yehova atayamba kulenga zinthu, mwacikondi anasankha kupatsa zolengedwa zake zaluntha ufulu wosankha zocita. Woyamba kupatsidwa mphatso imeneyi anali Mwana wake woyamba kubadwa, amene ni “cifanizilo ca Mulungu wosaonekayo.” (Akol. 1:15) Ngakhale poyamba Yesu ali kumwamba, anasankha kukhala wokhulupilika kwa Atate wake, ndi kukana kugwilizana ndi cipanduko ca Satana. Komanso atabwela padziko lapansi, anaseŵenzetsa ufulu wake kukana mayeselo a Mdani wamkuluyo. (Mat. 4:10) M’pemphelo lake locokela pansi pa mtima, usiku wakuti maŵa lake aphedwa, Yesu anatsimikiza kuti sadzasunthika pa cifunilo ca Mulungu. Iye anati: “Atate, ngati mukufuna, ndicotseleni kapu iyi. Komatu cifunilo canu cicitike, osati canga.” (Luka 22:42) Tiyeni titengele citsanzo ca Yesu coseŵenzetsa ufulu wathu kulemekeza Yehova ndi kucita cifunilo cake. Koma kodi n’zothekadi zimenezi?

5 Inde, n’zotheka. Cifukwa cake n’cakuti, mofanana ndi Yesu, ifenso tinalengedwa m’cifanizilo ca Mulungu. (Gen. 1:26) Koma pali malile. Tilibe ufulu wonse umene Yehova ali nawo. Mau a Mulungu amaonetsa kuti ufulu wathu uli na polekezela, ndipo sitiyenela kulumpha malile amene Yehova anatiikila. Mwacitsanzo, akazi afunika kugonjela amuna awo, ndipo ana afunika kugonjela makolo. (Aef. 5:22; 6:1) Kodi timacita bwanji tikafika pa malile amenewo? Yankho la funso limeneli lingakhudze tsogolo lathu lonse.

KUKWANITSA KAPENA KULEPHELA KUSEŴENZETSA BWINO UFULUWO

6. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti m’pake ufulu wathu kukhala na malile.

6 Kodi ufulu wokhala ndi malile ni ufulu weni-weni? Yankho ni INDE! N’cifukwa ciani tatsindika conco? Malile amenewo ni citetezo. Mwacitsanzo, tili na ufulu woyendetsa motoka kupita kutali ku mzinda waukulu. Koma bwanji ngati pofika mu mzindamo mupeza kuti mulibe malamulo a pamsewu. Aliyense ali na ufulu wothamangitsa motoka mmene angafunile, kapena kuyendela kumbali iliyonse ya msewu. Kodi mungacite mantha? Kwambili! Conco, malile ni ofunikila kuti tonse tisangalale na ufulu weni-weni. Kuti tionenso bwino pagona nzelu yosalumphila malile amene Yehova anaika pa ufulu wathu, tiyeni tioneko zitsanzo zina za m’Baibo.

7. (a) Kodi mphatso ya ufulu wosankha zocita inamusiyanitsa bwanji Adamu ku zolengedwa zina mu Edeni? (b) Fotokozani mmene Adamu anaseŵenzetsela ufulu wake wocita zinthu.

7 Mulungu polenga munthu woyamba, Adamu, anam’patsa mphatso ya ufulu wosankha zocita imenenso anapatsa angelo kumwamba. Ici cinasiyanitsa Adamu ndi nyama. Izo zimangocita zinthu mwacibadwa. Ganizilani mmene Adamu anaseŵenzetsela ufulu wake m’njila yoyenela. Nyama zinalengedwa munthu asanalengedwe. Koma Yehova anasungila mwana wake waumunthu woyamba, mwayi wopatsa zinyama maina. Mulungu “anayamba kuzibweletsa kwa munthuyo, kuti ciliconse aciche dzina.” Adamu anali kuyang’anitsitsa nyama iliyonse ndi kuipatsa dzina loyenelela. Ndipo Yehova sanali kuloŵelelapo n’kupelekanso maina ake ayi. Koma “dzina lililonse limene munthuyo anachula camoyo ciliconse, limenelo linakhaladi dzina lake.”—Gen. 2:19.

8. Kodi Adamu analephela bwanji kuseŵenzetsa bwino ufulu wake? Ndipo panakhala zotulukapo zanji?

8 Mwa tsoka lake, Adamu sanakhutile na nchito imene Mulungu anam’patsa yolima munda wa Edeni ndi kuusamalila. Sanakhutile ndi madalitso akuti: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile. Muyang’anilenso nsomba, . . . , zolengedwa zouluka . . . , komanso colengedwa ciliconse cokwawa padziko lapansi.” (Gen. 1:28) M’malomwake, iye anasankha kulumpha malile amene Mulungu anamuikila akuti asadye cipatso coletsedwa. Kulephela kuseŵenzetsa bwino ufulu kwa Adamu kunabweletsa mavuto osaneneka kwa mbadwa zake mpaka lelo. (Aroma 5:12) Zimenezi ziyenela kutithandiza kuseŵenzetsa mwanzelu ufulu wathu wosankha zocita, komanso mosapitilila malile amene Yehova anatiikila.

9. Ni ufulu wanji umene Yehova anapatsa anthu ake Aisiraeli? Nanga iwo anasankha ciani?

9 Mbadwa za a Adamu zinatengela ucimo ndi imfa kwa makolo awo osamvela. Koma sizinalandidwe mphatso ya ufulu wosankha zocita. Zimenezi zimaonekela ndi mmene Yehova anacitila ndi mtundu wa Aisiraeli. Kupitila mwa mtumiki wake Mose, Yehova anapatsa anthuwo mwayi wosankha kuvomeleza kapena kukana kukhala cuma cake capadela. (Eks. 19:3-6) Kodi iwo anasankha ciani? Anavomela kucita zonse zofunikila kwa anthu odziŵika ndi dzina la Mulungu. Capamodzi anafuula kuti: “Zonse zimene Yehova wanena tidzacita zomwezo.” (Eks. 19:8) Koma n’zacisoni kuti m’kupita kwa nthawi, mtunduwo unalephela kuseŵenzetsa bwino ufulu wawo, ndipo unaphwanya lonjezo lawo limenelo. Tiyeni titengelepo phunzilo pa citsanzo coipa cimeneci. Tiicengete bwino mphatso yathu ya ufulu wosankha zocita, mwa kukangamila kwa Yehova, ndi kuyendela mfundo zake zolungama.—1 Akor. 10:11.

10. N’zitsanzo ziti zotionetsa kuti n’zotheka anthu opanda ungwilo kulemekeza Mulungu ndi ufulu wawo? (Onani pikica yakuciyambi.)

10 Mu caputa 11 ya Aheberi, tipezamo maina 16 a atumiki a Mulungu amene anaseŵenzetsa ufulu wawo mosapitilila malile amene Yehova anaika. Cotulukapo cake n’cakuti, anapeza madalitso ambili, ndi ciyembekezo ca tsogolo lowala. Nowa mwacitsanzo. Anali wokhulupilika ndipo anasankha kulabadila malangizo a Mulungu omanga cingalawa copulumutsilamo banja lake, kutinso kukabadwe mibadwo ina m’tsogolo. (Aheb. 11:7) Abulahamu na Sara nawonso anatsatila citsogozo ca Mulungu kupita ku dziko lolonjezedwa. Ngakhale pamene anali kale mkati mwa ulendo wautali umenewu, anali nawo mpata kapena ufulu wobwelela ku mzinda wotukuka wa Uri. Koma m’malo mwake, iwo anangoika cikhulupililo cawo pa ‘kukwanilitsika kwa malonjezo’ a Mulungu. Anali ‘kufunitsitsa malo abwino koposa.’ (Aheb. 11:8, 13, 15, 16) Mose anafulatila cuma ca Aiguputo, “ndipo anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mocita zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zaucimo.” (Aheb. 11:24-26) Tiyeni titengele cikhulupililo ca atumiki amakedzana amenewa, cocengeta bwino mphatso yathu ya ufulu wosankha zocita, poigwilitsila nchito kucita cifunilo ca Mulungu.

11. (a) Kodi ufulu wocita zinthu umatipatsa dalitso lapadela liti? (b) Kodi colinga cathu kweni-kweni poseŵenzetsa bwino ufulu wosankha zocita n’ciani?

11 Ngakhale zingaoneke zacidule kupempha munthu wina kutisankhila zocita, kucita zimenezo n’kusayamikila dalitso limene tinapatsidwa. Dalitso limenelo lipezeka pa Deuteronomo 30:19, 20. (Ŵelengani.) Pa vesi 19 pali mwayi wosankha umene Mulungu anapatsa Aisiraeli. Vesi 20 ionetsa kuti Yehova anawapatsa mpata woonetsa zimene zinali m’mitima yawo. Ifenso tili na mwayi wosankha kulambila Yehova. Colinga cathu cacikulu poseŵenzetsa mphatso ya ufulu wocita zinthu, ndico kuonetsa cikondi cathu kwa Mulungu, ndi kuti ulemu ndi ulemelelo wonse zipite kwa iye.

PEWANI KUSEŴENZETSA UFULU WANU MOLAKWA

12. Tipeweletu kucita ciani ndi mphatso yathu yosankha zocita?

12 Yelekezani kuti munapatsa mnzanu mphatso yodula kwambili. Mungamve bwanji mutamva kuti iye anaitaya kudzala kapena m’bini, kapena kuti anaigwilitsila nchito kuvulaza munthu wina? Ndiye ganizilani mmene Yehova ndi mmene anthu ambili amaseŵenzetsela molakwika mphatso yawo ya ufulu wosankha zocita, ngakhale kuvulazila anthu ena. Baibo inakambilatu kuti “masiku otsiliza” anthu adzakhala “osayamika.” (2 Tim. 3:1, 2) Tiyeni tipewe kucita ciliconse coonetsa kusayamikila kapena kupeputsa mphatso yapadela yocokela kwa Yehova imeneyi. Kodi n’ziti maka-maka zofunika kupewa?

13. Monga Akhiristu, tingapewe bwanji kuseŵenzetsa molakwa ufulu wathu?

13 Tonse tili na ufulu wosankha anthu oceza nawo, mavalidwe, modzikonzela, ndi zosangalatsa. Komabe, ufulu wathu ungakhale “cophimbila zoipa” ngati timakhala akapolo a zilakolako za thupi lathu, kapena ngati timangotengela masitaelo onyazitsa a dziko lino. (Ŵelengani 1 Petulo 2:16.) M’malo moseŵenzetsa ufulu wathu ‘kulimbikitsa zilakolako za thupi,’ tifunika kusankha zinthu zotithandiza kulabadila cenjezo lakuti: “Citani zonse ku ulemelelo wa Mulungu.”—Agal. 5:13; 1 Akor. 10:31.

14. Kodi kudalila Yehova kungatithandize bwanji pankhani ya ufulu wathu?

14 Njila ina yotetezela ufulu wathu ni kudalila Yehova, na kum’lola kuti azitithandiza kusalumpha malile amene anatiikila. Iye yekha ndiye ‘amatiphunzitsa kuti zinthu zitiyendele bwino, amene amaticititsa kuti tiyende m’njila imene tiyenela kuyendamo.’ (Yes. 48:17) Tiyenela kudzicepetsa ndi kuvomeleza mfundo ya m’Mau a Mulungu yakuti: “Munthu wocokela kufumbi alibe ulamulilo wowongolela njila ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo wowongolela mapazi ake.” (Yer. 10:23) Conde, tisagwele mu msampa wodalila nzelu zathu, monga anacitila Adamu ndi Aisiraeli opanduka aja. M’malomwake, tiyeni ‘tikhulupilile Yehova ndi mtima [wathu] wonse.’—Miy. 3:5.

TIZILEMEKEZA UFULU WA ENA

15. Tiphunzilanji pa mfundo ya pa Agalatiya 6:5?

15 Mulungu amafunanso kuti tizilemekeza ufulu wa ena pa zosankha zawo. Cifukwa ciani? Cifukwa aliyense ali na ufulu wosankha zimene afuna. Zili conco kaya ni pa nkhani ya makhalidwe kapena kulambila. Kumbukani mfundo ya pa Agalatiya 6:5. (Ŵelengani.) Ngati tikumbukila mfundo yakuti Mkhiristu aliyense afunika “kunyamula katundu wake,” tidzalemekeza ufulu wa ena pa zosankha zawo.

M’bale akana mowa pa phwando

Tingapange zosankha zathu komanso kulemekeza ufulu wa ena (Onani palagilafu 15)

16, 17. (a) Kodi ufulu wosankha unakhala bwanji vuto kwa Akhiristu a ku Korinto? (b) Nanga Paulo anaitsiliza bwanji nkhaniyo? Ndipo tiphunzilapo ciani za ufulu wa ena?

16 Tiyeni tione citsanzo ca m’Baibo coonetsa kufunika kolemekeza ufulu wa abale pa nkhani zokhudza cikumbumtima. Akhiristu ku Korinto anayamba kugaŵikana cifukwa ca nkhani ya kudya nyama zimene zinali zopelekedwa nsembe ku mafano, koma pambuyo pake zinali kugulitsidwa pa maliketi. Ena anali kuganiza kuti: ‘Popeza fano ni cinthu copanda pake, munthu angadye nyamayo ndi cikumbumtima coyela.’ Koma ena amene poyamba anali olambila mafano anaona kuti kudya nyamayo ni kulambila fano. (1 Akor. 8:4, 7) Imeneyi inali nkhani yodetsa nkhawa, ndipo ikanatha kugaŵanitsa mpingo. Kodi Paulo anawathandiza bwanji Akhiristu a ku Korinto kukhala ndi kapenyedwe ka Mulungu pa nkhaniyo?

17 Coyamba, Paulo anakumbutsa magulu onse aŵili kuti cakudya sicingawapezetse ciyanjo ca Mulungu. ( 1 Akor. 8:8) Caciŵili, anawacenjeza kuti ‘ufulu wawo’ usakhale “copunthwitsa kwa ofooka.” (1 Akor. 8:9) Ndiyeno, analangiza aja amene anali na cikumbumtima cofooka kuti sayenela kuweluza anzawo amene anali kudya nyama imeneyo. (1 Akor. 10:25, 29, 30) Cotelo, pa nkhani yaikulu imeneyi yokhudza kulambila, Mkhiristu aliyense anafunika kupanga cosankha mogwilizana ndi cikumbumtima cake. Conco, ifenso tifunika kulemekeza ufulu wa ena pa zosankha zawo pa nkhani zaumwini.—1 Akor. 10:32, 33.

18. Mudzacita ciani poonetsa kuti mumayamikila mphatso ya ufulu wosankha zocita?

18 Yehova anatipatsa ufulu wosankha zocita, ndipo ndiwo ufulu weni-weni. (2 Akor. 3:17) Timaiyamikila ngako mphatso imeneyi cifukwa imatilola kupanga zosankha zoonetsa kuti Yehova timam’kondadi. Tisaleke kuyamikila mphatso yapadela imeneyi, mwa kuiseŵenzetsa polemekeza Mulungu, ndi mwa kulemekeza ufulu wa ena pa zosankha zawo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani