Zamkati
3 MBILI YANGA—Napindula Cifukwa Coyenda ndi Anthu Anzelu
WIKI YA MAY 1-7, 2017
8 Muzilemekeza Amene Afunika Kulandila Ulemu
Akhristu afunika kukhala na maganizo oyenela pankhani yopeleka ulemu. N’ndani amene ayenela kupatsidwa ulemu? Nanga n’cifukwa ciani? Nkhani ino itithandiza kuyankha mafunso amenewa, ndiponso ifotokoza mapindu amene tingapeze ngati tipeleka ulemu kwa amene ayenela kulandila ulemu.
WIKI YA MAY 8-14, 2017
13 Khalani ndi Cikhulupililo Ndipo Muzipanga Zosankha Mwanzelu
Baibo imatilimbikitsa kuti sitiyenela kukayika-kayika kapena kulephela kupanga zosankha. Kodi n’cifukwa ciani tifunika kupanga zosankha mwanzelu? Nanga n’ciani cingatithandize kucita zimenezo? Kodi m’poyenela nthawi zina kusintha zosankha zimene tinapanga kale? M’nkhani imeneyi tidzapeza mayankho a mafunso amenewa.
WIKI YA MAY 15-21, 2017
18 Tumikilani Yehova ndi Mtima Wathunthu
WIKI YA MAY 22-28, 2017
23 Kodi Mudzatengelapo Phunzilo pa Zimene Zinalembedwa?
Pokhala anthu opanda ungwilo, tonse timalakwitsa nthawi zina. Koma kodi zimenezi zitanthauza kuti sitingathe kukondweletsa Yehova? M’nkhani ziŵilizi tidzakambilana za mafumu anayi aciyuda ndi zolakwa zimene anacita. Zina mwa zolakwa zawo zinali zazikulu. Ngakhale n’conco, Yehova anaona kuti mafumuwo anali na mtima wathunthu. Nanga bwanji ife? Kodi Mulungu adzaona kuti tili na mtima wathunthu ngakhale kuti nthawi zina timalakwa?
28 Kukhalabe Bwenzi Pakacitika Zinthu Zimene Zingasokoneze Ubwenzi