Magazini Yophunzila
MARCH 2017
NKHANI ZOPHUNZILA: MAY 1-28, 2017
© 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
PIKICA YA PACIKUTO:
ROMANIAMkulu ameneyu ndi mkazi wake amaona kuti nthawi yabwino yolalikila kwa anthu onga nkhosa kumpoto kwa Romania, ndi pa Sondo, pambuyo pa misonkhano. Anthu amenewa aphatikizapo azimayi aŵili amene akukonza ubweya wa nkhosa.
OFALITSA
40,575
MAPHUNZILO A BAIBO
25,623
OPEZEKA PA CIKUMBUTSO (2015)
78,300
Magazini ino si yogulitsa. Colinga cake ni kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibo imene ikucitika padziko lonse lapansi. Ndalama zoyendetsela nchitoyi ni zimene anthu amapeleka mwa kufuna kwawo.
Ngati mufuna kupeleka ndalama zothandizila nchitoyi, yendani pa www.jw.org.
Baibo imene taseŵenzetsa ni Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kusiyapo ngati taonetsa ina. Komabe, ena mwa masipeling’i a Cinyanja m’magazini ino tatsatila malamulo a m’buku lakuti A Unified Standard Orthography for South-Central African Languages.