Zamkati
WIKI YA MAY 29, 2017–JUNE 4, 2017
3 ‘Muzikwanilitsa Zimene Mwalonjeza’
Kodi munapangapo malonjezo angati kwa Yehova? Limodzi, aŵili, kapena ambili? Kodi mumayesetsa kucita zinthu mogwilizana ndi malonjezo anu? Nanga bwanji ponena za lonjezo lanu la kudzipeleka kapena la cikwati? Nkhani ino, idzatikumbutsa citsanzo cabwino cimene Yefita ndi Hana anatipatsa pamene tiyesetsa kukwanilitsa zimene tinalonjeza kwa Mulungu.
WIKI YA JUNE 5-11, 2017
9 Kodi Cidzacokapo N’ciani Ufumu wa Mulungu Ukadzabwela?
Nthawi zambili timaganizila zimene Yehova adzaticitila m’Paradaiso. Koma m’nkhani ino, tidzakambilana zimene Mulungu adzacotsa padziko lapansi. Kodi Yehova adzacotsa ciani kuti padziko pakhale mtendele ndi cimwemwe? Kuganizila yankho la funso limeneli, kudzalimbitsa cikhulupililo cathu ndi kutithandiza kukhalabe opilila.
14 Mbili Yanga—N’natsimikiza Mtima Kukhala Msilikali wa Khristu
WIKI YA JUNE 12-18, 2017
18 Woweluza wa Dziko Lonse” Amacita Cilungamo Nthawi Zonse
WIKI YA JUNE 19-25, 2017
23 Kodi Mumacita Zinthu Mogwilizana ndi Cilungamo ca Yehova?
Tikaona kuti ife kapena munthu wina wacitilidwa zinthu zopanda cilungamo, cikhulupililo, kudzicepetsa, ndi kukhulupilika kwathu zingayesedwe. Nkhanizi zidzafotokoza zocitika zitatu za m’Baibo, zimene zidzatithandiza kucita zinthu mogwilizana ndi cilungamo ca Yehova.
WIKI YA JUNE 26, 2017–JULY 2, 2017
28 Yehova Atamandike Cifukwa ca Kudzipeleka Kwanu!
Yehova payekha ni wacikwane-kwane. Komabe, iye amakondwela akaona kuti tikuyesetsa kucilikiza ulamulilo wake. Oweruza macaputa 4 ndi 5, aonetsa kuti Yehova amayamikila ngati ticita modzipeleka zimene iye watilamula.