Magazini Yophunzila
April 2017
NKHANI ZOPHUNZILA: MAY 29–JULY 2, 2017
© 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
PIKICA YA PACIKUTO:
ZAMBIA
Mokondwela, abale na alongo a m’kagulu ka ulaliki acoka pa Nyumba ya Ufumu kupita muulaliki ku Lusaka, muno mu Zambia. Nyumba ya Ufumu yosamalidwa bwino imeneyi yacititsa anthu kutamanda Yehova
OFALITSA
183,586
MAPHUNZILO A BAIBO
415,706
OPEZEKA PA CIKUMBUTSO (2016)
782,527
Magazini ino si yogulitsa. Colinga cake ni kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibo imene ikucitika padziko lonse lapansi. Ndalama zoyendetsela nchitoyi n’zimene anthu amapeleka mwa kufuna kwawo.
Ngati mufuna kupeleka ndalama zothandizila nchitoyi, yendani pa www.jw.org.
Baibo imene taseŵenzetsa ni Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kusiyapo ngati taonetsa ina. Komabe, ena mwa masipeling’i a Cinyanja m’magazini ino tatsatila malamulo a m’buku lakuti A Unified Standard Orthography for South-Central African Languages.