Zamkati
WIKI YA JULY 3-9, 2017
3 Kuthandiza Alendo Ocokela ku Mayiko Ena “Kutumikila Yehova Mokondwela”
WIKI YA JULY 10-16, 2017
8 Kuthandiza Ana a Alendo Ocokela m’Dziko Lina
Nkhani yoyamba idzafotokoza mavuto amene abale na alongo othaŵa kwawo amakumana nawo, na zimene ife tingacite kuti tiwathandize. Nkhani yaciŵili idzafotokoza mmene mfundo za m’Baibo zingathandizile makolo amene akukhala m’dziko lina kupanga zosankha zimene zingapindulitse ana awo.
13 Mbili Yanga—Kukhala Wogontha Sikunanilepheletse Kuphunzitsa Ena
WIKI YA JULY 17-23, 2017
17 Musalole Kuti Cikondi Canu Cizilale
WIKI YA JULY 24-30, 2017
22 “Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”
Kukhala m’dziko loipali ni cinthu covuta kwa mtumiki wa Yehova aliyense. Nkhani izi, zidzafotokoza mmene tingapewele mzimu wodzikonda wa m’dzikoli mwa kupitilizabe kukonda Yehova, Baibo, ndi abale athu. Zidzafotokozanso zimene tingacite kuti tizikonda kwambili Khristu osati zinthu za m’dzikoli.
27 Mmene Gayo Anathandizila Abale Ake