LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w17 May masa. 31-32
  • “Cangu na Cikondi Cathu Zinawonjezeka Kwambili”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Cangu na Cikondi Cathu Zinawonjezeka Kwambili”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
w17 May masa. 31-32
Khamu la anthu ladzala m’ciholo cacikulu pa msonkhano wacigawo ku Cedar Point, Ohio, mu 1922

ZA M’NKHOKWE YATHU

“Cangu na Cikondi Cathu Zinawonjezeka Kwambili”

PACISANU m’maŵa, mu September 1922, anthu okwana 8,000 anakhamukila m’ciholo cacikulu. Panthawiyo kunja kunali kutayamba kale kutentha. Cheyamani analengeza kuti m’cigaŵo cimeneci, aliyense ni wololedwa kutuluka m’holoyo, koma palibe amene adzaloledwa kungenanso.

M’sonkhanowo unayamba na nyimbo zotamanda Mulungu. Pambuyo pake, M’bale Joseph F. Rutherford anapita kukaimilila pa pulatifomu. Ambili pamsonkhanowo anali na cidwi ngako cofuna kumvetsela. Ena ocepa anali kuyenda-yenda cifukwa kunali kotentha. Mkambi anawapempha kuti akhale pansi kuti amvetsele nkhani. Nkhaniyo itayamba, palibe amene anadziŵa kuti m’mwamba kutsogolo kwa pulatifomu kunali cinsalu copindidwa bwino.

M’bale Rutherford anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Ufumu wa kumwamba wayandikila.” Iye anakamba nkhaniyi pafupi-fupi ola limodzi na hafu. Mau ake amphamvu anali kumveka m’holo yonseyo pamene anali kufotokoza mmene aneneli akale analengezela mopanda mantha za Ufumu umene ukubwelawo. Pamene nkhaniyi inafika pacimake, M’bale Rutherford anafunsa kuti, “Kodi mukhulupilila kuti Mfumu yaulemelelo yayamba kulamulila?” Anthu onse pamsonkhanowo anayankha mokweza kuti: “Inde!”

Ndiyeno M’bale Rutherford anafuula kuti: “Ndiye pitani mukalalikile, inu ana a Mulungu wam’mwamba-mwamba! Onani, Mfumu yayamba kale kulamulila ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza ufumuwo. Conco lengezani, lengezani, lengezani Mfumu ndi ufumu wake.”

Panthawi imeneyo, cinsalu copinda cimene cinali ku pulatifomu cinatambasuliwa, ndipo panali mau akuti: “Lengezani Mfumu ndi ufumu wake.”

Ray Bopp anati: “Anthu pamsonkhanowo anakondwela ngako.” Komanso mlongo Anna Gardner anakamba kuti “mtenje unanjenjemela mwamphamvu cifukwa abale na alongo anaomba m’manja kwambili na cisangalalo.” Nayenso M’bale Fred Twarosh anati: “Onse pamsonkhanowo anaimilila panthawi imodzi.” M’bale winanso, dzina lake Evangelos Scouffas, anati: “Zinali monga kuti cinthu cina cake camphamvu catinyamula tonse pamipando yathu. Tinaimilila ndipo m’maso mwathu munadzala misozi yacisangalalo.”

Ambili pamsonkhanowo anali atayamba kale kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Koma panthawiyo analimbikitsidwa kuwonjezela cangu cawo. Ethel Bennecoff anakamba kuti pamene Ophunzila Baibulo anabwelela kumanyumba kwawo, ‘cangu na cikondi [cawo] zinawonjezeka kwambili.’ Odessa Tuck, amene panthawiyo anali na zaka 18, atacoka pamsonkhanowo anatsimikiza mtima kukhala wodzipeleka monga Yesaya. Iye anati: “Sin’nali kudziŵa kumene nidzapita kukatumikila, utumiki umene nidzacita, kapena mmene nidzaucitila. Koma n’nali wofunitsitsa kukhala monga Yesaya, amene anati: ‘Ine ndilipo! Nditumizeni.’” (Yes. 6:8) M’bale Ralph Leffler anakamba kuti “Tsiku limenelo linali ciyambi ceni-ceni ca nchito yolengeza Ufumu imene yafalikila padziko lonse lapansi.”

N’zosadabwitsa kuti msonkhano wacigawo umenewu, umene unacitika mu 1922 ku Cedar Point, Ohio, wakhala wosaiŵalika m’mbili ya atumiki a Mulungu. M’bale George Gangas anati, “Msonkhanowu unanicititsa kukhala na colinga cakuti nisadzaphonye msonkhano uliwonse.” Ndipo kuyambila nthawiyo, iye sanaphonyekodi msonkhano uliwonse. Komanso mlongo Julia Wilcox analemba kuti: “Siningakwanitse kufotokoza cimwemwe cimene nimakhala naco nthawi iliyonse ngati m’mabuku athu akambamo za msonkhano umene unacitika ku Cedar Point mu 1922. Nthawi zonse nimayamikila Yehova cifukwa conipatsa mwayi wopezekapo.’”

Ambili a ise timakumbukila msonkhano wacigawo umene unatisangalatsa ndi kutilimbikitsa kukhala wacangu, ndiponso kukonda kwambili Mulungu wathu wamkulu ndi Mfumu yake. Tikakumbukila nthawi yokondweletsa imeneyo, naise timalimbikitsidwa kukamba kuti, “Zikomo kwambili Yehova cifukwa conipatsa mwayi wopezekapo.”

Zilembo Zacinsinsi

Pamsonkhanowo, zilembo zakuti “ADV” (zimene mau ake amatanthauza “kulengeza” m’Cizungu) zinali kupezeka paliponse—pamitengo, pa zipupa za nyumba, ngakhalenso pa pulogilamu ya msonkhano. Anthu pamsonkhanowo anali na cidwi cofuna kudziŵa tanthauzo lake.a

Pakhomo lililonse ndi pa zipilala anamatapo makhadi oyela okhala na zilembo zikulu-zikulu zakuda zakuti ADV. Tinafunsa kuti zilembozo zinali kutanthauza ciani, koma zinaoneka kuti panalibe amene anali kudziŵa. Ngati ena anali kudziŵa, sanatiuze.”—Edith Brenisen.

a Mpaka pano zilembozi n’zacinsinsi m’lingalilo lakuti zithunzi zake sizinapezekebe.

Zinatheka Cifukwa Pemphelo Lawo Linayankhidwa

Arthur ndi Nellie Claus anafika msanga pamsonkhano kuti apeze malo abwino okhala. Arthur anati: “N’nali kumvetsela nkhani mwachelu.” Koma mwadzidzidzi, iye anamva m’mala kuŵaŵa. Arthur anakakamizika kutuluka m’holoyo, olo kuti anadziŵa kuti sadzaloledwa kungenanso. Kalinde ananifunsa kuti, “N’cifukwa ciani mukucoka pa nthawi yofunika ngati ino?” Koma Arthur anaona kuti afunika kucoka ndithu.

Pamene anali kubwelako, Arthur anamvela anthu m’holoyo akuomba m’manja mwamphamvu ndi mwacikondwelelo. Conco, anayamba kusakila cibowo kunja kwa holoyo kuti amveleko zimene zinali kucitika m’katimo. Posakila-sakila, anapeza malo abwino okwelela, ndipo anakwela holoyo mpaka kufika ku mtenje, pamwamba potalika mamita 4.8 kucoka pansi. Ali kumtenjeko, anapita pa malo ena owala bwino okhala na mawindo otsegula.

Kumeneko, Arthur anapeza abale angapo amene anathedwa nzelu, ndipo anali kungoyang’anitsitsa mkambi. Iwo anali atauzidwa kuti ajuŵe nthambo zingapo panthawi imodzi kuti cisalu cokhala na mau citambasuke. Koma panapelewela mpeni umodzi kuti akwanitse kucita zimenezi. Kodi Arthur anali na mpeni? Inde anali nawo, ndipo abalewo atadziŵa, mitima yawo inakhala pansi. Arthur na anzakewo anakhala m’malo awo n’kumayembekezela cizindikilo cowadziŵitsa kuti adule nthambozo. Iwo anauzidwa kuti M’bale Rutherford akakamba kaciŵili mau akuti “Lengezani!” afunika kujuŵa nthambozo.

Abale na alongo amene anaona cocitikaci, anakamba kuti cinsalu cacikulu cimeneco ca mitundu itatu cinatambasuka bwino-bwino, ndipo pakati pake panali cithunzi ca Yesu.

Pambuyo pake, abalewo anafotokozela Arthur kuti pokwela pamtenjepo, anaseŵenzetsa makwelelo, ndiyeno makwelelowo anacotsedwapo. Conco, zinali zovuta kuti atsike kukapempha mpeni wina. Iwo anali kungopemphela kwa Yehova kuti atumize m’bale amene ali na mpeni. Abalewo sanakayikile ngakhale pang’ono kuti Yehova anayankha pemphelo lawo m’njila yocititsa cidwi kwambili.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani