Umoyo Wosalila Zambili Umabweletsa Cimwemwe
DANIEL NA MIRIAM anakwatilana mu September 2000, ndipo anali kukhala mu mzinda wa Barcelona, m’dziko la Spain. Daniel anati: “Tinali na umoyo umene anthu m’dzikoli amaona kuti ndiwo umoyo wabwino ngako. Popeza tinali kugwila nchito yapamwamba, tinali kugula zakudya m’malestilanti apamwamba, kuyenda ku mayiko ena, ndi kugula zovala zodula. Komanso, tinali kulalikila mokhazikika.” Koma pambuyo pake zinthu zinasintha.
Pa msonkhano wacigawo mu 2006, panakambiwa nkhani imene inam’fika pamtima Daniel. M’nkhaniyo, munali funso lakuti: “Kodi tikuchita zomwe tingathe pothandiza omwe ‘akuyenda movutikira popita kukaphedwa’ kuti abwere pa njira ya kumoyo wosatha?” (Miy. 24:11) Nkhaniyo inagogomeza kwambili za udindo wathu wolalikila uthenga wa m’Baibo wopulumutsa moyo. (Mac. 20:26, 27) Daniel anakamba kuti: “N’namvela monga kuti Yehova akukamba na ine.” Nkhaniyo inakambanso kuti kuwonjezela utumiki kumabweletsa cimwemwe coculuka. Daniel anadziŵa kuti zimenezi zinali zoona, cifukwa mkazi wake Miriam anali atayamba kale kucita upainiya, ndipo anali kukhala wosangalala.
Daniel anati: “N’naona kuti nifunika kusintha zambili paumoyo wanga.” Iye anasinthadi. Anacepetsa nthawi yoseŵenza n’kuyamba kucita upainiya. Cinanso, anaganizila za cimwemwe cimene iye na mkazi wake angapeze ngati apita kukatumikila kumene kuli olengeza Ufumu ocepa.
POYAMBA ZINALI ZOVUTA, KENAKO UTHENGA WOKONDWELETSA
Mu May 2007, Daniel na Miriam, analeka kuseŵenza, n’kupita ku dziko la Panama, kumene m’mbuyomu, anapita kukayenda. Gawo lawo latsopano linali zisumbu za ku Bocas del Toro ku Nyanja ya Caribbean. Anthu ambili okhala m’zisumbuzi ndi a mtundu wa Guaymi, ndipo ndiwo nzika za delali. Daniel na Miriam anali kuganiza kuti ndalama zimene anasunga zidzawathandiza potumikila m’dziko la Panama kwa miyezi pafupi-fupi 8.
Daniel na mkazi wake anali kukwela boti pocoka pa cisumbu cina kupita pa cina, ndipo akafika pa cisumbu anali kukwela njinga. Iwo akumbukila zimene zinacitika paulendo wawo woyamba. Anayenda mtunda wa makilomita 32 pa njinga, kudutsa m’vikweza ndi m’misondo, dzuŵa lili phwee! Daniel anatsala pan’gono kukomoka cifukwa colema. Komabe, anthu aciguami, amene nyumba zawo zinali m’mbali mwa njila anali kuwalandila bwino, maka-maka pamene anadziŵako mau ena m’citundu cawo. Posakhalitsa, iwo anayamba kucititsa maphunzilo a Baibo okwanila 23.
Komabe, ndalama zimene anasunga zitatha, cimwemwe cawo cinasanduka cisoni. Daniel anati: “Tinali kufuna kulila tikaganizila zobwelela kwathu ku Spain. Tinali kukwinyilila tikaganizila kuti tidzasiya maphunzilo athu a Baibo.” Koma patangopita mwezi umodzi, iwo analandila uthenga wokondweletsa. Miriam anati: “Tinauzidwa kuti tiyambe kutumikila monga apainiya apadela. Tinakondwela ngako kudziŵa kuti tidzapitiliza utumiki wathu.”
CIMENE AMAKONDWELA NACO NGAKO
Cifukwa ca kusintha kwa zinthu m’gulu kumene kunacitika mu 2015, Daniel na Miriam anauzidwa kuti azitumikila monga apainiya anthawi zonse osati apadela. Kodi iwo anacitanji? Anakhulupilila lonjezo la pa Salimo 37:5, pamene pamati: “Lola kuti Yehova akutsogolele panjila yako, umudalile ndipo iye adzacitapo kanthu.” Iwo anapeza nchito kuti azipeza zofunikila paumoyo wawo pocita upainiya. Ndipo lomba atumikila mumpingo wina m’cigawo ca Veraguas, m’dziko la Panama.
Daniel anati: “Tikalibe kucoka ku Spain, sitinali kudziŵa kuti tidzakwanitsa kukhala na umoyo wosalila zambili. Koma lomba timakwanitsa. Sitisoŵa ciliconse cofunika paumoyo.” Kodi n’ciani maka-maka cimene cimawakondweletsa? Iwo anati, “Cimwemwe cimene timakhala naco pothandiza anthu odzicepetsa kudziŵa Yehova, sitingaciyelekezele na cina ciliconse.”