Zamkati
3 Anadzipeleka na Mtima Wonse—Ku Turkey
WIKI YA AUGUST 28, 2017–SEPTEMBER 3, 2017
Nkhani iyi idzafotokoza mmene tingaseŵenzetsele cuma cathu kuti ‘tidzipezele mabwenzi’ kumwamba. (Luka 16:9) Idzafotokozanso mmene tingapewele kukhala akapolo kwa anthu amalonda m’dzikoli, komanso zimene tingacite kuti titumikile Yehova mokwanila.
WIKI YA SEPTEMBER 4-10, 2017
12 “Lilani Ndi Anthu Amene Akulila”
Kodi Mkhristu angapilile bwanji imfa ya munthu amene anali kum’konda? Yehova amapeleka citonthozo ca panthawi yake kupitila mwa Yesu Khristu, Malemba, ndi mpingo wacikhristu. Nkhaniyi idzafotokoza mmene ise tingapezele citonthozo, ndiponso mmene tingatonthozele ena amene afedwa.
WIKI YA SEPTEMBER 11-17, 2017
17 N’cifukwa Ciani Tifunika Kutamanda Yehova?
Salimo 147 imalimbikitsa anthu a Mulungu mobweleza-bweleza kuti afunika kutamanda Yehova. N’zinthu ziti zokhudza Yehova zimene zinapangitsa wolemba salimoyi kuona kuti Mulungu ni wofunika kutamandidwa? Nkhani iyi idzafotokoza zinthu zimenezo. Idzafotokozanso cifukwa cake na ise tifunika kukhala ofunitsitsa kutamanda Mulungu wathu.
WIKI YA SEPTEMBER 18-24, 2017
22 Mulungu “Akwanilitse Zofuna Zanu”
Abale na alongo ambili acicepele ayamba utumiki wa nthawi zonse. Kodi n’zimenenso imwe mufuna? Nkhani iyi ipeleka malangizo abwino ocokela m’Malemba, amene adzakuthandizani kukhala na zolinga zabwino zimene zingakuthandizeni kuti mtsogolo, mudzakhale na umoyo wabwino ndi wacimwemwe.