Zamkati
WIKI YA SEPTEMBER 25, 2017–OCTOBER 1, 2017
3 Kodi Mudzayembekezela Moleza Mtima?
WIKI YA OCTOBER 2-8, 2017
8 “Mtendele wa Mulungu . . . Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse”
Nkhani yoyamba idzafotokoza cifukwa cake tifunika kuyembekezela Yehova. Tidzakambilananso zimene tingaphunzile kwa amuna ndi akazi okhulupilika akale pankhani yombekezela Mulungu moleza mtima. Nkhani yaciŵili idzaonetsa mmene Yehova nthawi zina amacitila zinthu m’njila imene sitinali kuyembekezela. Kukambilana zimenezi kudzalimbitsa cikhulupililo cathu mwa iye pamene tiyembekezela moleza mtima kuti atithandize pa mavuto athu.
13 Mbili Yanga Kupilila Ziyeso Kumabweletsa Madalitso
WIKI YA OCTOBER 9-15, 2017
17 Mmene Timavulila Umunthu Wakale ndi Kusauvalanso
WIKI YA OCTOBER 16-22, 2017
22 Mmene Timavalila Umunthu Watsopano ndi Kusauvulanso
Nkhani yoyamba idzafotokoza zimene kuvula umunthu wakale kumatanthauza na cifukwa cake tifunika kucita zimenezi mwamsanga. Idzafotokozanso zimene tingacite kuti tipewe kubwelelanso ku umunthu wakale. Nkhani yaciŵili idzafotokoza makhalidwe angapo amene ali mbali ya umunthu watsopano. Idzafotokozanso mmene tingaonetsele makhalidwe amenewa mu umoyo wathu wa tsiku na tsiku ndi muulaliki.