Yophunzila
DECEMBER 2017
NKHANI ZOPHUNZILA: JANUARY 29–FEBRUARY 25, 2018
© 2017 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
PIKICA YA PACIKUTO:
CÔTE D’IVOIRE
Dziko la Côte d’Ivoire (limene kale linali kuchedwa Ivory Coast) ndiye kumene amalima kwambili nyemba za koko, zimene amapangila cokoleti. Nyembazi amaziyanika pa dzuwa kuti ziume. Mpainiya akulalikila uthenga wofunika kwambili wa m’kabuku kakuti Uthenga Wabwino, kwa munthu amene akuyanika nyemba za koko
OFALITSA
11,133
MAPHUNZILO A BAIBO
28,274
OPEZEKA PA CIKUMBUTSO (2016)
76,526
Magazini ino si yogulitsa. Colinga cake ni kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibo imene ikucitika padziko lonse lapansi. Ndalama zoyendetsela nchitoyi n’zimene anthu amapeleka mwa kufuna kwawo.
Ngati mufuna kupeleka ndalama zothandizila nchitoyi, yendani pa www.jw.org.
Baibo imene taseŵenzetsa ni Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kusiyapo ngati taonetsa ina. Komabe, ena mwa masipeling’i a Cinyanja m’magazini ino tatsatila malamulo a m’buku lakuti A Unified Standard Orthography for South-Central African Languages.