Mau Oyamba
KODI MULUNGU AMAKUDELANI NKHAWA?
Masoka aakulu akacitika kapena pamene anthu avutika na kufa, tingadzifunse ngati Mulungu amaona komanso kukhudzidwa na zimenezi. Baibo imakamba kuti:
“Pakuti maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzelo lawo, koma nkhope ya Yehova imakwiyila anthu ocita zoipa.”—1 Petulo 3:12.
Nsanja ya Mlonda ino, ionetsa mmene Mulungu amatithandizila komanso zimene akucita kuti acotsepo mavuto onse.