MBILI YANGA
Zinthu Zonse N’zotheka kwa Yehova
“IMFA siidzakhalaponso ndipo akufa adzakhalanso na moyo.” Mkazi wanga, Mairambubu anamva mau amenewa pamene anali m’basi pa ulendo. Iye anakhala na cidwi cofuna kudziŵa zambili. Basi itaima, anthu anayamba kutsika. Nthawi yomweyo, Mairambubu anathamangila mzimayi amene anakamba mau amenewo. Mzimayiyo dzina lake anali Apun Mambetsadykova, ndipo anali wa Mboni za Yehova. Masiku amenewo, kukamba na Mboni za Yehova kunali koopsa. Koma zimene tinaphunzila kwa Apun zinasinthilatu umoyo wathu.
KUSEŴENZA KUYAMBILA M’MAŴA MPAKA MADZULO
N’nabadwa mu 1937, ku mafamu a kufupi na mzinda wa Tokmok m’dziko la Kyrgyzstan. Banja lathu ni la mtundu wacikigizi ndipo timakamba cikigizi. Makolo anga anali kugwila nchito pa famu, kuyambila m’maŵa mpaka madzulo. Ogwila nchito ku mafamu nthawi na nthawi anali kupatsidwa cakudya, koma anali kulandila malipilo awo kamodzi pa caka. Amayi anali kuvutika posamalila ine na mlongosi wanga wamng’ono. Sukulu n’nalekeza giledi 5, ndipo n’nayamba kuseŵenza pa famu.
Mapili a Teskey Ala-Too
M’dela limene n’nali kukhala, umphawi unali paliponse ndipo kuti munthu apeze zofunikila pa umoyo anali kufunika kugwila nchito zolimba. Popeza n’nali wacicepele, sin’nali kuganizila kwambili za colinga ca moyo kapena za tsogolo. Sin’nali kudziŵa kuti coonadi camtengo wapatali cokamba za Yehova Mulungu na colinga cake cidzasintha kwambili umoyo wanga. Nkhani ya mmene coonadi cinafikila m’dziko la Kyrgyzstan na kufalikila ndi yocititsa cidwi kwambili. Cinayambila kwathu kweni-kweni, kumpoto kwa dziko la Kyrgyzstan.
OTHAMANGITSIDWA KWAWO ANABWELETSA COONADI KU KYRGYZSTAN
Coonadi cokamba za Yehova Mulungu cinayamba kuzika mizu m’dziko la Kyrgyzstan ca m’ma 1950. Kuti izi zitheke, Mboni zinalimbana ndi ndale za mphamvu zacikomyunizimu. Motani? Dziko limene lomba limachedwa Kyrgyzstan linali pansi pa ulamulilo wa Soviet Union. Mboni za Yehova zimene zinali m’maiko onse olamulidwa na Soviet Union, sizinali kutengako mbali m’zocitika zandale. (Yoh. 18:36) Mwa ici, iwo anali kudedwa ndi kuzunzidwa na boma la Soviet Union. Koma ndale sizinalepheletse Mau a Mulungu kufikila anthu oona mtima. Imodzi mwa mfundo zofunika kwambili zimene naphunzila mu umoyo wanga ni yakuti, “zinthu zonse n’zotheka” kwa Yehova.—Maliko 10:27.
Emil Yantzen
Kuzunzidwa kwa Mboni za Yehova kunacititsa kuti ciŵelengelo cawo ciwonjezeke ku Kyrgyzstan. Motani? Ulamulilo wa Soviet Union unaphatikizapo cigawo ca Siberia, kumene adani a Boma anali kutumizidwa monga akaidi. Pamene akaidiwo anamasulidwa, ambili anabwela m’dziko la Kyrgyzstan, ndipo ena mwa iwo anabwela na coonadi. Mmodzi mwa iwo anali Emil Yantzen, amene anabadwila ku Kyrgyzstan mu 1919. Emil anali atatumizidwa ku ndende, ndipo kumeneko anakumana na Mboni. Iye anaphunzila coonadi ndipo anabwelako mu 1956. Emil anayamba kukhala pafupi na mudzi wochedwa Sokuluk m’dela lathu. Ku Sokuluk n’kumene kunakhazikitsidwa mpingo woyamba m’dziko la Kyrgyzstan. Umu munali m’caka ca 1958.
VictorVinter
Patapita caka cimodzi Victor Vinter anakukila ku Sokuluk. M’bale wokhulupilika ameneyu anakumana na zovuta mobwelezabweleza. Kaŵili konse anamangidwa ndi kuikidwa m’ndende kwa zaka zitatu cifukwa cokana kutengako mbali m’zandale. Ndiyeno pambuyo pake, anapika jele zaka zina 10. Komanso anatumizidwa ku dziko lina lakutali, kukakhala monga mkaidi kwa zaka 5. Ngakhale n’conco, cizunzo sicinaletse kufalikila kwa coonadi.
COONADI CINAFIKA KUFUPI NA KWATHU
Eduard Varter
Kudzafika mu 1963, m’dziko la Kyrgyzstan munali Mboni pafupi-fupi 160. Ambili a iwo anali ocokela ku Germany, Ukraine, na ku Russia. Mmodzi wa iwo anali Eduard Varter. Iye anabatizika mu 1924 ku Germany. M’ma 1940, Boma la Nazi linam’tumiza ku ndende yozunzilako anthu. Pambuyo pa zaka zingapo, boma la Soviet Union linam’tumiza ku dziko lina lakutali, kukakhala monga mkaidi. Mu 1961, m’bale wokhulupilika ameneyu anakukila ku tauni ya Kant, imene ili pafupi kwambili na kwathu.
Elizabeth Fot; Aksamai Sultanalieva
Nayenso Elizabeth Fot, mtumiki wokhulupilika wa Yehova anali kukhala ku Kant. Iye anali kupeza zofunikila za mu umoyo wake mwa kugwila nchito yosoka zovala. Cifukwa cakuti anali wa luso pa nchito yake, anthu olemekezeka monga madokota na matica anali kusoketsa zovala kwa iye. Mmodzi wa makasitoma ake anali Aksamai Sultanalieva, amene anali mkazi wa loya wa boma. Aksamai anapita kwa Elizabeth kukasoketsa zovala. Iye anafunsa Elizabeth mafunso ambili okhudza colinga ca moyo komanso mkhalidwe wa akufa. Elizabeth anam’yankha mafunso ake poseŵenzetsa Baibo. Aksamai anakhala mlaliki wokangalika wa uthenga wabwino.
Nikolai Chimpoesh
Ca pa nthawi imeneyi, m’bale Nikolai Chimpoesh, amene anacokela ku Moldova, anaikidwa kukhala woyang’anila dela. Iye anatumikila pa udindowu kwa zaka pafupi-fupi 30. Nikolai sanali kungocezela mipingo koma analinso kuyang’anila nchito yocita fotokope zofalitsa na kuzitumiza ku mipingo. Akulu-akulu a Boma anazindikila nchito imene iye anali kucita. Mwa ici, Eduard Varter anapatsa Nikolai malangizo olimbikitsa akuti: “Ngati akulu-akulu a boma akufunsa kumene timatenga zofalitsa zathu, mosapita mbali uziŵayankha kuti timazitenga ku likulu lathu ku Brooklyn. Ndipo uzimuyang’ana pamaso wapolisiyo. Suyenela kuopa ciliconse.”—Mat. 10:19.
Atatsiliza kukambilana, sipanapite nthawi yaitali kuti Nikolai aitanidwe ku likulu la apolisi, ku tauni ya Kant. Nikolai anatifotokozela zimene zinacitika. Iye anati “Wapolisi ananifunsa kumene timatenga zofalitsa zathu ndipo ine n’namuuza kuti timazitenga ku Brooklyn. Wapolisiyo anasoŵa coyankha. Anangonilola kupita, ndipo kucokela nthawiyo sananiitanenso.” Mboni zopanda mantha monga zimenezi zinapitiliza kulalikila uthenga wabwino mosamala m’cigawo ca kwathu, ku mpoto kwa Kyrgyzstan. Coonadi ca mtengo wapatali cokamba za Yehova, cinafika m’banja langa mu 1981. Mkazi wanga Mairambubu, ndiye anali woyamba kumva coonadi.
MOFULUMILA MKAZI WANGA ANAZINDIKILA COONADI
Kwawo kwa Mairambubu ni ku dela lochedwa Naryn, m’dziko la Kyrgyzstan. Tsiku lina mu August 1974, iye anabwela ku nyumba ya mlongosi wanga, ndipo kumeneko n’kumene tinakumana. N’tangomuona, n’nam’konda kwambili, cakuti tinakwatilana tsiku lomwelo.
Apun Mambetsadykova
Mu January 1981, pamene Mairambubu anali m’basi paulendo wopita ku msika, anamvetsela zokamba za mzimayi uja amene nachula kuciyambi. Mkazi wanga anafunitsitsa kudziŵa zambili. Conco, anapempha mzimayiyo kuti amudziŵitse dzina na adresi yake. Mzimayiyo anati dzina lake ni Apun. Koma anali kucita zinthu mosamala cifukwa olo m’ma 1980, nchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa. Conco, m’malo mopatsa mkazi wanga adresi yake, iye ndiye anatenga yathu. Mkazi wanga anabwela ku nyumba ali wosangalala.
Mairambubu ananiuza kuti, “Namva zinthu zokondweletsa kwambili. Mkazi wina waniuza kuti posacedwa anthu sadzafanso. Akuti ngakhale zilombo za kusanga zidzakhala pa mtendele na anthu.” Kwa ine, izi zinali monga nthano ndipo n’nati, “Tiye tiyembekezele mpaka abwele kukatifotokozela zambili.”
Apun anabwela kudzaticezela patapita miyezi itatu. Pambuyo pake, alongo enanso anayamba kubwela kudzaphunzila nase. Mwanjila imeneyi, tinadziŵana ndi Mboni zina zoyambilila za mtundu wacikigizi. Alongowo anatiphunzitsa coonadi ca mtengo wapatali cokamba za Yehova na colinga cake kwa anthu. Anatiŵelengela buku lakuti, Kucokera ku Paradaiso Wotaika Kumka ku Paradaiso Wopezedwanso.a Cifukwa cakuti bukuli linali limodzi mu mzinda wonse wa Tokmok, tinali kucita kukopela na manja kuti tikhale nalo.
Cimodzi mwa zinthu zoyambilila zimene tinaphunzila, ni ulosi wa pa Genesis 3:15. Ulosiwu udzakwanilitsidwa kupitila mwa Yesu, Mfumu yodzozedwa na Mulungu. Uthenga umenewu ni wofunika ngako, ndipo anthu onse afunika kuumva! Izi zinatilimbikitsa kuyamba kugwila nawo nchito yolalikila. (Mat. 24:14) Pasanapite nthawi, coonadi ca m’Baibo cinayamba kusintha miyoyo yathu.
MISONKHANO NA UBATIZO PA NTHAWI YA CILETSO
M’bale wina wa ku Tokmok anatiitanila ku phwando la cikwati. Ine na mkazi wanga tinazindikila kuti Mboni zimacita zinthu mosiyana ndi ena. Pa phwando limenelo panalibe moŵa, ndipo linali ladongosolo. Izi zinali zosiyana kwambili na maphwando ena acikwati amene tinapitako. Kumeneko, oitainidwa anali kuledzela, kucita zinthu zina zoipa, na kukamba mau onyoza.
Tinalinso kupezeka pa misonkhano ina yacikhristu mu mpingo wa ku Tokmok. M’nyengo yotentha, misonkhano tinali kucitikila kusanga. Abale na alongo anali kudziŵa kuti apolisi anali kutilondalonda. Conco, m’bale mmodzi anaikidwa kuti akhale kalinde. M’nyengo yozizila, tinali kucitila m’nyumba misonkhano. Kangapo konse, apolisi anabwela ku nyumbayo. Iwo anali kufuna kudziŵa zimene tinali kucita. Pa tsiku limene ine na Mairambubu tinabatizika mu Mtsinje wa Chüy, mu July 1982, tinayesetsa kukhala osamala. (Mat. 10:16) Patsikulo, abale anali kubwela kusanga m’tumagulu tung’onotung’ono kuti asonkhane. Titasonkhana, tinaimba nyimbo ya Ufumu, ndipo kenako tinamvetsela nkhani ya ubatizo.
TINAONA KUTI UNALI MWAYI WOWONJEZELA UTUMIKI WATHU
Mu 1987, m’bale wina ananipempha kuti nikaonane ndi munthu winawake wacidwi amene anali kukhala m’tauni ya Balykchy. Kucokela kwathu kukafika kumeneko, ulendo wa pa sitima unali kutenga maola anayi. Pambuyo polalikila maulendo angapo ku Balykchy, tinazindikila kuti m’tauniyo munali anthu ambili acidwi. Umenewu unalidi mwayi wakuti tionjezele utumiki wathu.
Kaŵili-kaŵili, ine na Mairambubu tinali kupita ku Balykchy. Nthawi zambili, pa Ciŵelu na pa Sondo tinali kukhala kumeneko. Tinali kupita mu ulaliki na kucititsa misonkhano. Ciŵelengelo ca anthu ofuna zofalitsa zathu cinawonjezeka kwambili. Tinali kunyamula zofalitsa kucokela ku Tokmok kupita nazo ku Balykchy. Tinali kuzinyamulila mu saka yonyamulilamo mbatatisi, yochedwa mishok. Zofalitsa zodzala masaka aŵili zinali kutha mwezi umodzi cabe. Tinalinso kulalikila m’sitima popita ku Balykchy na pobwela.
Mu 1995, mpingo woyamba unakhazikitsidwa m’tauni ya Balykchy. Izi zinacitika patapita zaka 8 kucokela pa ulendo woyamba umene tinapita kukalalikila m’tauniyo. Panafunika ndalama zambili kuti tikwanitse kuyenda maulendo onsewo ocoka ku Tokmok kupita ku Balykchy. Popeza tinali osauka, kodi tinakwanitsa bwanji kucita zimenezi? M’bale wina anali kutipatsa ndalama zolipilila zinthu zina. Yehova anaona kuti tinali ofunitsitsa kucita zambili mu utumiki, conco anatitsegulila “zipata za kumwamba” ndi kutikhuthulila madalitso. (Mal. 3:10) Ndithudi, zinthu zonse n’zotheka kwa Yehova!
KUTANGWANIKA POSAMALILA BANJA NA UTUMIKI
Mu 1992, n’naikidwa kuti nizitumikila monga mkulu, ndipo n’nali m’bale woyamba wacikigizi kukhala mkulu mu Kyrgyzstan. Mu mpingo wathu wa ku Tokmok, tinakhala na mwayi wocitako mautumiki ena. Tinali kuphunzila Baibo ndi acicepele ambili acikigizi amene anali kucita maphunzilo awo pa makoleji a m’delalo. Mmodzi wa acicepelewo tsopano akutumikila m’Komiti ya Nthambi, ndipo ena aŵili ni apainiya apadela. Tinalinso kuyesetsa kuthandiza ena pa misonkhano yathu. Cakumayambililo kwa zaka za m’ma 1990, zofalitsa zathu zinali za Cirasha, ndiponso misonkhano inali kucitika m’Cirasha. Koma ambili mu mpingo wathu anali kukamba Cikigizi. Conco, n’nali kucita kumasulila nkhani za m’Cirasha kuti abale amvetse coonadi mosavuta.
Ine, mkazi wanga na ana athu 8 mu 1989
Ine na Mairambubu tinalinso otangwanika posamalila banja lathu limene linali kukula. Tinali kutenga ana athu popita mu ulaliki na ku misonkhano ya mpingo. Mwana wathu wamkazi Gulsayra, amene pa nthawiyo anali na zaka 12, anali kukonda kulalikila anthu opita na njila. Komanso, ana athu anali kukonda kusunga Malemba pa mtima. Mwa njila imeneyi, iwo ndi adzukulu athu anali kutengako mbali mokwanila pa zinthu zauzimu. Pali pano, tili ndi ana 9 na adzukulu 11. Mwa amenewa, 16 akutumikila Yehova ndipo adzukulu athu aang’ono amasonkhana na makolo awo.
KUPITA PATSOGOLO KWA COONADI
Abale na alongo okondedwa amene anayamba nchito ya Yehova m’dela lathu ca m’ma 1950, angasangalale kuona mmene coonadi capitila patsogolo. Kuyambila m’ma 1990, takhala tikusangalala kwambili na ufulu wolalikila uthenga wabwino na kusonkhana pamodzi mwaunyinji.
Ine na mkazi wanga tili mu ulaliki
Mu 1991, ine na mkazi wanga tinapezekapo pa msonkhano wacigawo woyamba umene unacitikila mu mzinda wa Alma-Ata, umene lomba umachedwa kuti Almaty ku Kazakhstan. Ndipo mu 1993, abale mu Kyrgyzstan anacita msonkhano wacigawo woyamba mu sitediyamu ya Spartak mu mzinda wa Bishkek. Abale na alongo anayeletsa sitediyamu imeneyi, wiki yonse msonkhano usanafike. Woyang’anila sitediyamu, anakondwela ngako cakuti anatilola kucitilamo msonkhano popanda malipilo.
Cinthu cosaiŵalika n’cakuti mu 1994, zofalitsa zathu zinayamba kupulintiwa m’citundu ca Cikigizi. Tsopano zofalitsa zimamasulidwa m’Cikigizi ndi kagulu ka omasulila amene ali pa ofesi ya nthambi ku Bishkek. Mu 1998, nchito ya Mboni za Yehova inavomelezedwa mwalamulo mu Kyrgyzstan. Tsopano gulu lathu lakula, cakuti ciŵelengelo ca ofalitsa cipitilila 5,000. Masiku ano, tili na mipingo 83 na tumagulu 25 tumene tumacita misonkhano m’Cichainizi, Cizungu, Cikigizi, Cirasha, Cinenelo ca Manja ca ku Russia, Citeki, Ciwiga, na Ciuzibeki. Abale na alongo ocokela kosiyana-siyana amenewa, amatumikila Yehova mogwilizana. Ni Yehova amene wacititsa kuti kupita patsogolo kumeneku kutheke.
Yehova anasinthilatu umoyo wanga. N’nakulila m’banja la alimi osauka, ndipo n’naphunzila kwa zaka 5 cabe. Koma Yehova wanithandiza kutumikila monga mkulu na kuphunzitsa anthu ophunzila kwambili kuti adziŵe coonadi ca mtengo wapatali. Inde, Yehova amacititsa kuti zinthu zooneka monga zosatheka zitheke. Zocitika za mu umoyo wanga zimanisonkhezela kupitiliza kulengeza za Yehova, amene kwa iye “zinthu zonse n’zotheka.”—Mat. 19:26
a Lofalitsidwa na Mboni za Yehova, koma lomba analeka kulipulinta.