Zamkati
WIKI YA APRIL 30, 2018–MAY 6, 2018
3 Ubatizo Ni Wofunika kwa Mkhristu Aliyense
WIKI YA MAY 7-13, 2018
8 Makolo, Kodi Mukuthandiza Ana Anu Kupita Patsogolo Kuti Akabatizike?
Kodi colinga cathu ciyenela kukhala ciani pamene tiphunzitsa munthu Baibo? N’cifukwa ciani kuwayawaya kubatizika n’kulakwa? N’cifukwa ciani makolo ena acikhristu amalimbikitsa ana awo kuti asabatizike mwamsanga? M’nkhani ziŵilizi, tidzakambilana mafunso amenewa na ena.
13 Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
WIKI YA MAY 14-20, 2018
14 Kucelezana ni Khalidwe Lofunika Kwambili
Mtumwi Petulo anauza Akhristu a m’nthawi yake kuti: “Muzicelezana popanda kudandaula.” (1 Pet. 4:9) N’cifukwa ciani kucelezana n’kofunika ngako masiku ano? Kodi anthu ena tingawaceleze m’njila ziti? Nanga tingaonetse bwanji kuti ndise alendo abwino? M’nkhani iyi, tidzakambilana mafunso amenewa.
19 Mbili Yanga Yehova Sananigwilitse Mwala
WIKI YA MAY 21-27, 2018
23 Cilango Ni Umboni Wakuti Mulungu Amatikonda
WIKI YA MAY 28, 2018–JUNE 3
28 “Mvelani Malangizo Kuti Mukhale Anzelu”
Nkhani izi zidzatithandiza kuyamikila kwambili cikondi cacikulu cimene Mulungu amationetsa mwa kutipatsa cilango monga Tate wathu. Koma kodi Mulungu amatipatsa bwanji cilango? Nanga tifunika kucita ciani akatipatsa cilango? Funso lina n’lakuti, tingacite ciani kuti tizitha kudzilanga tekha? Mayankho a mafunso amenewa ali m’nkhani ziŵili zimenezi.