Zamkati
WIKI YA AUGUST 6-12, 2018
3 “Ufumu Wanga Suli Mbali ya Dziko Lino”
WIKI YA AUGUST 13-19, 2018
8 Tikhale Amodzi, Monga Mmene Yehova na Yesu Alili Amodzi
Anthu m’nthawi ya Yesu anali ogaŵikana cifukwa cosiyana pa zandale, cikhalidwe, kapena mitundu. M’nkhani ziŵilizi, tidzaphunzila mmene Khristu anaphunzitsila otsatila ake kuti akhale ogwilizana na kupewa tsankho limene limagaŵanitsa anthu. Tidzaphunzilanso mmene tingatengele citsanzo cawo m’dziko logaŵikanali.
WIKI YA AUGUST 20-26, 2018
16 Lolani Malamulo a Mulungu na Mfundo Zake Kuphunzitsa Cikumbumtima Canu
Kuti cikumbumtima cathu cizititsogolela bwino, tifunika kuciphunzitsa. Mwacikondi, Yehova anatipatsa malamulo na mfundo zimene zingatithandize kuphunzitsa bwino cikumbumtima cathu na kuona zinthu mmene iye amazionela. Nkhaniyi idzafotokoza mmene tingaseŵenzetsele bwino mfundo za m’Baibo mu umoyo wathu.
WIKI YA AUGUST 27, 2018–SEPTEMBER 2, 2018
21 “Onetsani Kuwala Kwanu” Kuti Yehova Alemekezeke
Yesu analimbikitsa ophunzila ake kuti ayenela kuonetsa kuwala kwawo kuti Mulungu alemekezeke. Nkhaniyi idzafotokoza malangizo abwino amene tikawaseŵenzetsa angatithandize kuonetsa kuwala kwathu mokwanila.