Zamkati
WIKI YA DECEMBER 31, 2018–JANUARY 6, 2019
3 “Gula Coonadi Ndipo Usacigulitse”
WIKI YA JANUARY 7-13, 2019
8 “Ndidzayenda M’coonadi Canu”
Nkhani ziwilizi zidzatilimbikitsa kuti tiziyamikila coonadi camtengo wapatali cimene Yehova watiphunzitsa. Coonadi cimeneci n’camtengo wapatali kuposa zinthu zilizonse zimene tinatailapo kuti ticipeze. Tidzakambilananso zimene tingacite kuti tipitilize kuona coonadi kukhala camtengo wapatali, komanso kuti tisacigulitse kapena kunyalanyaza mfundo zina za coonadi cimene Yehova watiphunzitsa.
WIKI YA JANUARY 14-20, 2019
13 Dalilani Yehova Kuti Mukhalebe na Moyo
Buku la Habakuku lionetsa zimene tingacite kuti tipitilize kudalila Yehova pamene tikumana na mavuto. Nkhani iyi idzatithandiza kuona kuti tikakhala na nkhawa kapena ngati tikukumana na mavuto kapena ziyeso, tifunika kudalila Mulungu. Tikatelo, iye adzatithandiza kupilila.
WIKI YA JANUARY 21-27, 2019
18 Kodi Mumayendela Maganizo a Ndani?
WIKI YA JANUARY 28, 2019–FEBRUARY 3, 2019
23 Kodi Mumayesetsa Kuona Zinthu Mmene Yehova Amazionela?
Pamene tikula mwauzimu, timayamba kuona kuti kaonedwe ka zinthu ka Yehova ndiko kabwino koposa. M’nkhani ziwilizi tidzakambilana zimene tingacite kuti tipewe kuyendela maganizo a dzikoli, na kuwongola maganizo athu kuti tiziona zinthu mmene Yehova amazionela.
28 Kukoma Mtima—Khalidwe Limene Limaonekela M’mawu na M’zocita