Zamkati
WIKI YA FEBRUARY 4-10, 2019
Akhristu oona amayembekezela mwacidwi kukakhala M’paradaiso. Nkhaniyi idzafotokoza umboni wamphamvu wa M’malemba wotsimikizila kuti Paradaiso adzakhalako. Idzafotokozanso tanthauzo la mawu amene Yesu anakamba polonjeza Paradaiso.
8 Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
WIKI YA FEBRUARY 11-17, 2019
10 Muzilemekeza “Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi”
Nkhaniyi idzafotokoza zimene Baibo imakamba ponena za cikwati colemekezeka. Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza cikwati? Nanga tingaonetse bwanji kuti timayendela malangizo a m’Baibo pa nkhani ya cisudzulo na kupatukana?
15 Mbili Yanga—‘Yehova Waticitila Zinthu Zabwino’
WIKI YA FEBRUARY 18-24, 2019
19 Acicepele, Mlengi Wanu Amafuna Kuti Mukhale Acimwemwe
WIKI YA FEBRUARY 25, 2019–MARCH 3, 2019
24 Acicepele, Mungakhale na Umoyo Wacimwemwe
Acicepele nthawi zambili amafunika kupanga zosankha zazikulu. Mwacitsanzo, angafunike kudziikila zolinga zoti adzazikwanilitse mu umoyo. Kaŵili-kaŵili anthu amalimbikitsa acicepele kucita maphunzilo apamwamba kapena kupeza nchito yapamwamba. Koma Yehova amalangiza acicepele kuti ayenela kuika iye patsogolo mu umoyo. Nkhani ziŵilizi zidzatithandiza kuona kuti kumvela Mulungu ndiye cinthu canzelu.
29 “Wolungama Adzakondwela mwa Yehova”
32 Mlongoza Nkhani wa Magazini a 2018 a Nsanja ya Mlonda na Galamuka!