LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp19 na. 2 masa. 12-13
  • Mukafika Pakuti Simufunanso Kukhala na Moyo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mukafika Pakuti Simufunanso Kukhala na Moyo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMENE MUNGAPEZE THANDIZO
  • KODI MATENDA OVUTIKA MAGANIZO ADZATHA?
  • Kodi Baibo Inganithandize Ngati Nili na Maganizo Ofuna Kudzipha?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
  • 2 | “Malemba . . . Amatilimbikitsa”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
wp19 na. 2 masa. 12-13
Agwila Baibo m’manja pa thebulo, ndipo ayang’ana kutsogolo mwacidwi

Mukafika Pakuti Simufunanso Kukhala na Moyo

Mkazi wina wa ku Brazil dzina lake Adriana anati: “Matenda amenewa sanaleke kunivutitsa. Conco, n’naona kuti cingakhale bwino kuti nidziphe cabe.”

KODI NA IMWE munavutikapo maganizo cakuti simunafunenso kukhala na moyo? Ngati n’conco, ndiye kuti mungamvetse mmene Adriana anamvelela. Iye anam’peza na matenda ovutika maganizo. Adriana anali kuvutika kwambili na nkhawa, kukhala wokhumudwa, komanso kudzimva wopanda pake.

Ganizilaninso za mwamuna wina wa ku Japan dzina lake Kaoru, amene anali kusamalila makolo ake okalamba amene anali kudwala-dwala. Iye anati: “Panthawiyo, n’nali kukhala wopanikizika kwambili kunchito. M’kupita kwa nthawi, cifuno cakuti nidye cinatha. Ndiponso n’nali kuvutika kugona. N’naona kuti cingakhale bwino kufa cabe kuti nipumuleko mavuto.”

Mwamuna wina wa ku Nigeria dzina lake Ojebode, anati: “Nthawi zonse n’nali kukhala wokhumudwa, cakuti n’nali kulila. Conco n’nayesa kupeza njila yakuti nidziphe cabe.” Cokondweletsa n’cakuti Ojebode, Kaoru, komanso Adriana sanadziphe. Koma caka ciliconse anthu pafupi-fupi 800,000 amadzipha.

KUMENE MUNGAPEZE THANDIZO

Ambili amene amadzipha ni amuna. Ndipo ambili a iwo anali kucita manyazi kupempha thandizo. Yesu anati anthu odwala afunikila dokotala. (Luka 5:31) Conco, ngati muli na maganizo ofuna kudzipha, conde musacite manyazi kupempha thandizo. Ambili amene akudwala matenda a maganizo, apeza kuti thandizo la ku cipatala limawathandiza kuti amveleko bwino, na kuti apilile vuto lawo. Ojebode, Kaoru, komanso Adriana, onse analandila cithandizo ca mankhwala, ndipo tsopano amvelako bwino.

Madokotala angapeleke mankhwala, kapena kungokambilana na munthu wovutika maganizo. Kapenanso kuseŵenzetsa njila zonse ziŵili. Amene akudwala matenda amenewa, amafuna kuti acibululu komanso anzawo aziwamvetsetsa, kuleza nawo mtima, kuwakonda na kuwathandiza. Bwenzi labwino ngako limene munthu angakhale nalo ni Yehova Mulungu. Iye amapeleka thandizo labwino kupitila m’Mawu ake, Baibo.

KODI MATENDA OVUTIKA MAGANIZO ADZATHA?

Nthawi zambili, anthu ovutika maganizo angafunike kulandila cithandizo kwa nthawi itali. Angafunikenso kudziŵa mmene angapililile vutolo, mwa kusintha zinthu zina mu umoyo wawo. Ngati mukuvutika na matenda a maganizo, mungayembekezele tsogolo labwino monga Ojebode. Iye anati: “Niyembekezela mwacidwi kuona kukwanilitsidwa kwa Yesaya 33:24, imene imakamba za nthawi pamene padziko lonse lapansi, palibe adzakamba kuti ‘Ndikudwala.’” Monga Ojebode, pezani citonthozo m’lonjezo la Mulungu lokhudza “dziko lapansi latsopano,” mmene simudzakhalanso ‘zopweteka.’ (Chivumbulutso 21:1, 4) Lonjezo limeneli likadzakwanilitsidwa, kuvutika maganizo kulikonse kudzathelatu mpaka kale-kale. Zokuvutitsani maganizo “sizidzakumbukilidwanso ndipo sizidzabwelanso mumtima [mwanu].”—Yesaya 65:17.

Mavesi a m’Baibo Amene Angakuthandizeni

Mulungu amadziŵa bwino mmene mumvelela.

“Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwila dzanja lako lamanja, . . ndikukuuza kuti, ‘Usacite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’” —Yesaya 41:13.

Yehova amadziŵa bwino mmene timamvelela kuposa munthu wina aliyense, ndipo amafuna kutithandiza.

Sinkha-sinkhani pa Mawu a Mulungu.

“[Eliya] anayamba kupempha kuti afe, ponena kuti: ‘ . . . Cotsani moyo wanga Yehova.’”—1 Mafumu 19:4.

Ojebode anati: “Kusinkha-sinkha pa Mawu a Mulungu kunanithandiza. N’nadziŵa kuti mneneli Eliya nayenso panthawi ina, anamvela monga mmene n’namvelela ine.”

Phunzilani ku zitsanzo za m’Baibo.

“Ine [Yesu] ndakupemphelela iwe [Petulo] kuti cikhulupililo cako cisathe.”—Luka 22:32.

Pambuyo pakuti mtumwi Petulo wakana Yesu katatu, anavutika maganizo maningi, ndipo analila kwambili. Kaoru anati: “Cocitika ca Petulo cinanithandiza kuona kuti Yehova na Yesu, anamvetsa mmene Petulo anali kumvelela. Izi zinanilimbikitsa.”

Zokuvutitsani maganizo “sizidzakumbukilidwanso ndipo sizidzabwelanso mumtima [mwanu].”—Yesaya 65:17

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani