Zina Zimene Zilipo Pa Jw.Org
Kuyambila na magazini ino, Nsanja ya Mlonda idzayamba kuonetsa mitu ya nkhani zatsopano, zolinganako na zimene kale zinali kutuluka m’magazini athu. Nkhanizi zipezeka pa webusaiti yathu ya, jw.org.
MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA
Mungatani kuti Musamakwiye Mopitirira Malire?
Kukwiya kungawononge thanzi lanu. Nakonso kubisa mkwiyo kungakubweletseleni mavuto. Kodi mungacite ciani kuti musamakwiye mopitilila malile mukakumana ndi zocitika zokhumudwitsa?
(Pitani ku Chichewa, pa mbali yakuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANTHU OKWATIRANA KOMANSO MABANJA.)
BAIBULO LIMASINTHA ANTHU
Misewu Ndi Imene Inali Nyumba Yanga
Antonio anali kukonda kucita zaciwawa, kuseŵenzetsa am’kolabongo, na kumwa moŵa mwaucakolwa, moti anali kuona kuti moyo wake ni wopanda phindu. Kodi n’ciani cinamuthandiza kusintha?
(Pitani ku Chichewa, pa mbali yakuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MTENDERE KOMANSO MOYO WOSANGALALA.)