LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w19 January tsa. 31
  • Ciwalo Catsopano ca Bungwe Lolamulila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ciwalo Catsopano ca Bungwe Lolamulila
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Nkhani Zofanana
  • M’bale Watsopano wa m’Bungwe Lolamulila
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Ziwalo Ziŵili Zatsopano za Bungwe Lolamulila
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Kodi Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova N’ciyani?
    Mafunso Ofunsidwa Kaŵili-kaŵili pa Mboni za Yehova
  • Ziwalo Ziwili Zatsopano za Bungwe Lolamulila
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
w19 January tsa. 31
Kenneth and Jamie Cook

M’bale Kenneth E. Cook, Jr., na mkazi wake, Jamie

Ciwalo Catsopano Ca Bungwe Lolamulila

PA Citatu kuseni, pa January 24, 2018, a m’banja la Beteli ku America komanso ku Canada, anamvela cilengezo cokondweletsa cakuti M’bale Kenneth Cook, Jr waikidwa kukhala ciwalo catsopano ca Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova.

M’bale Cook anabadwila ku Pennsylvania, m’dziko la America, ndiponso n’kumene anakulila. Iye anaphunzila coonadi kwa mnzake wa kusukulu, atatsala pang’ono kutsiliza maphunzilo ake a kusekondale. Ndipo anabatizika pa June 7, 1980. M’baleyu anayamba upainiya wanthawi zonse pa September 1, 1982. Atacita upainiya kwa zaka ziŵili, anaitanidwa kuti akatumikile pa Beteli ya ku Wallkill, mu mzinda wa New York. Iye anayamba utumiki wake wa pa Beteli pa October 12, 1984.

Kwa zaka 25 kucokela nthawiyo, M’bale Cook anali kugwila nchito zosiya-siyana. Anaseŵenzelako kopulintila mabuku na ku dipatimenti yoyang’anila atumiki apa Beteli. Mu 1996, M’bale Cook anakwatila mlongo Jamie, ndipo anayamba kutumikila limodzi pa Beteli ku Wallkill. Mu December 2009, M’bale na Mlongo Cook anatumizidwa kukatumikila ku Likulu la Maphunzilo la Watchtower ku Patterson, mu mzinda wa New York. Kumeneko, M’baleyu anayamba kutumikila m’Dipatimenti Yoyankha Makalata. Ndiyeno, iwo anabwelelanso ku Wallkill, kumene anatumikilako kwa kanthawi kocepa. Kenako, mu April 2016, anawatumiza ku Brooklyn, mu mzinda wa New York. Patapita miyezi 5, anakukila ku likulu lathu la padziko lonse ku Warwick, mu mzinda wa New York. Ndipo mu January 2017, M’bale Cook anaikidwa kukhala wothandizila Komiti Yoona za Nchito Yolemba Mabuku ya Bungwe Lolamulila.

Tsopano m’Bungwe Lolamulila muli abale 8 odzozedwa.

Maina awo ni aya: K. E. Cook, Jr.; S. F. Herd; G. W. Jackson; M. S. Lett; G. Lösch; A. Morris III; D. M. Sanderson; D. H. Splane

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani