Ziwalo Ziwili Zatsopano za Bungwe Lolamulila
PA OCTOBER 5, 2024, pa msonkhano wapacaka panapelekedwa cilengezo capadela cakuti: M’bale Jody Jedele ndi M’bale Jacob Rumph aikidwa kukhala ziwalo za Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova. Abale awiliwa atumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka zambili.
Jody Jedele ndi mkazi wake, Damaris
M’bale Jedele anabadwila ku Missouri, ku America, ndipo analeledwa m’coonadi. Banja lao linali kukhala pafupi ndi gao losafoledwa kawili-kawili. Izi zinacititsa kuti adziwane ndi abale ocokela kumadela osiyana-siyana amene anali kupita kumaloko kukalalikila uthenga wabwino. Iye analimbikitsidwa ataona cikondi ndi mgwilizano pakati pao. Anabatizika pa October 15, 1983 ali ndi zaka pakati pa 13 ndi 14. Anali kukonda kulalikila, ndipo atamaliza maphunzilo a ku sekondale, anayamba upainiya wa nthawi zonse mu September 1989.
M’bale Jedele ali wacinyamata, makolo ake anali kukonda kum’tenga limodzi ndi mlongo wake kukaona malo ku Beteli. Maulendowa analimbikitsa anawo kudziikila colinga cokatumikila pa Beteli, ndipo anacikwanilitsadi. M’bale Jedele anafika pa Beteli ya ku Wallkill mu September 1990. Atafika ku Beteli, nchito yake yoyamba inali m’Dipatimenti Yoyeletsa. Pambuyo pake anagwila nchito m’Dipatimenti ya Zacipatala.
Pa nthawi imeneyo, mipingo yapafupi yolankhula ci Spanish inali kukula ndipo inali kufunikila abale. Conco, M’bale Jedele anayamba kugwilizana ndi umodzi mwa mipingoyo ndiponso anayamba kuphunzila ci Spanish. Posakhalitsa, anakumana ndi Damaris, mlongo amene anali kucita upainiya m’delalo. Kenako anakwatilana, ndipo mlongoyo nayenso anayamba kutumikila pa Beteli.
Mu 2005, iwo anacoka pa Beteli kuti akasamalile makolo ao. Pa nthawi imene anali kusamalila makolowo, iwo anali kucitanso upainiya wa nthawi zonse. M’bale Jedele anacititsapo Sukulu ya Utumiki wa Upainiya, ndipo anatumikilapo m’Komiti Yokambilana ndi Acipatala, komanso m’Komiti Yomanga ya Cigao.
Mu 2013, M’bale ndi Mlongo Jedele anaitanidwanso ku Beteli kuti akathandize pa nchito yamamangidwe ya ku Warwick. Kungocokela nthawiyo, iwo atumikilako ku Patterson ndi ku Wallkill. M’bale Jedele watumikilapo m’Dipatimenti ya Zamamangidwe ndi mu Ofesi Yothandiza pa Zacipatala. Mu March 2023, anaikidwa kukhala wothandiza Komiti ya Utumiki. Poganizila mautumiki amene iye wacitapo, M’baleyu anati: “Nthawi zina ukapatsidwa utumiki watsopano, umacita mantha. Koma zikakhala telo m’pamene umafunika kudalila Yehova, cifukwa iye amaticititsa kuti tikwanitse kucita ciliconse cimene afuna.”
Jacob Rumph ndi mkazi wake, Inga
M’bale Rumph anakulila mu mzinda wa California, ku America. Ali mwana, amai ake anayesetsa kum’phunzitsa coonadi ca m’Baibo ngakhale kuti iwo anali ozilala. Caka ciliconse, anali kukonda kukaona ambuye ake, amene anali Mboni yokhulupilika. Ambuye akewo anam’thandiza kuti azikonda coonadi, ndipo ali ndi zaka 13 anapempha kuti ayambe kuphunzila Baibo. Pa September 27, 1992, anabatizika akali wacicepele. N’zokondweletsa kuti amai ake anayambanso kulalikila komanso kupezeka pa misonkhano, ndipo atate ake komanso azibale ake anayamba kupita patsogolo mwauzimu ndipo anabatizika.
M’bale Rumph ali wacicepele anali kuona kuti apainiya anali acimwemwe. Conco, atatsiliza sukulu anayamba upainiya mu September 1995. Mu 2000, anasamukila ku Ecuador kukatumikila ku malo osowa. Kumeneko anakumana ndi mlongo wina wa ku Canada amene anali mpainiya, dzina lake Inga, kenako anakwatilana. Atakwatilana, anayamba kukhala m’tauni ina ya ku Ecuador mmene munali kagulu kakang’ono ka ofalitsa. Masiku ano, m’tauniyi muli mpingo waukulu.
Patapita nthawi, M’bale ndi Mlongo Rumph anaikidwa kukhala apainiya apadela, ndipo pambuyo pake anayamba nchito ya m’dela. Mu 2011, anaitanidwa kukalowa kalasi ya nambala 132 ya Sukulu ya Giliyadi. Atamaliza maphunzilo, anatumikilako ku maiko osiyana-siyana, ndipo anacitako mautumiki monga utumiki wa pa Beteli, utumiki wa umishonale, ndi nchito ya m’dela. M’bale Rumph anakhalako ndi mwai wokhala mlangizi wa Sukulu ya Alengezi a Ufumu.
Cifukwa ca mlili wa COVID-19, M’bale ndi Mlongo Rumph anabwelela ku America. Iwo anaitanidwa ku Beteli ya ku Wallkill, kumene M’bale Rumph anaphunzitsidwa nchito ya mu Service Department. M’kupita kwa nthawi, anatumizidwanso ku nthambi ya ku Ecuador kumene M’bale Rumph anayamba kutumikila m’Komiti ya Nthambi. Mu 2023, anasamutsidwila ku ofesi ya nthambi ya ku Warwick. Ndiyeno mu January 2024, M’bale Rumph anaikidwa kukhala wothandizila Komiti ya Utumiki. Poganizila konseko kumene anatumikila, M’bale Rumph anati, “Cimene cimapangitsa utumiki kukhala wofunika kwenikweni si malo kumene ukutumikila, koma anthu amene ukutumikila nao.”
Timawayamikila zedi abalewa pogwila nchito mwakhama, ndipo “timawalemekeza kwambili.”—Afil. 2:29.