M’bale Watsopano wa m’Bungwe Lolamulila
M’mamawa pa Citatu, pa September 5, 2012, mabanja a Beteli a ku United States ndi ku Canada analandila cilengezo cakuti, m’bale wina anaikidwa kukhala membala watsopano wa Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova. M’bale Mark Sanderson anayamba kutumikila monga membala wa Bungwe Lolamulila pa September 1, 2012.
M’bale Sanderson anakulila ku San Diego, California, U.S.A. Iye analeledwa ndi makolo ake a Mboni, ndipo anabatizika pa February 9, 1975. Anayamba kutumikila monga mpainiya ku Saskatchewan, m’dziko la Canada, pa September 1, 1983. Mu December 1990, anamaliza maphunzilo ake m’kalasi ya nambala 7 ya Sukulu Yophunzitsa Utumiki, (imene panthawi ino imachedwa kuti Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Abale Osakwatila) ku United States. Mu April 1991, M’bale Sanderson anaikidwa kuti akatumikile monga mpainiya wapadela ku cilumba ca Newfoundland, ku Canada. Pambuyo potumikila monga woyang’anila dela wogwilizila, anaitanidwa kukhala membala wa banja la Beteli la ku Canada, mu February 1997. M’caka ca 2000, m’mwezi wa November, iye anasamutsidwa kupita ku nthambi ya ku United States. Kumeneko anali kutumikila m’Ofesi Yothandiza pa Zacipatala, ndiyeno pambuyo pake m’Dipatimenti ya Utumiki.
Mu September 2008, M’bale Sanderson analoŵa Sukulu ya Abale a m’Komiti ya Nthambi, ndipo pambuyo pake anaikidwa kukhala membala wa Komiti ya Nthambi ku Philippines. Mu September 2010, iye anaitanidwa kuti apitenso ku United States. Kumeneko anayamba kugwila nchito yothandiza Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulila.
[Cithunzi papeji 8]
[Bokosi papeji 8]
Abale Amene Ali M’bungwe Lolamulila Panthawi Ino
M’zela wakumbuyo, kuyambila kumanzele kupita kulamanja:
D. H. Splane, A. Morris III, D. M. Sanderson, G. W. Jackson, M. S. Lett. M’zela wakutsogolo, kuyambila kumanzele kupita kulamanja: S. F. Herd, G. Lösch, G. H. Pierce. Abale onse a m’Bungwe Lolamulila ndi Akristu odzozedwa