LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • jl phunzilo 22
  • Kodi ku Ofesi ya Nthambi Kumacitika Nchito Yanji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi ku Ofesi ya Nthambi Kumacitika Nchito Yanji?
  • Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Nkhani Zofanana
  • Njila Zowonjezela Utumiki Wanu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Nchito Yomanga Inayenda Bwino Mlili Usanayambe
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Oyang’anila Oweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
jl phunzilo 22

PHUNZILO 22

Kodi ku Ofesi ya Nthambi Kumacitika Nchito Yanji?

Abale akulinganiza nchito yokhudza ofesi ya nthambi ku Solomon Islands

Ku Solomon Islands

Mboni ya Yehova igwila nchito pa ofesi ya nthambi ku Canada

Ku Canada

Ma thilaki onyamula mabuku

Ku South Africa

A banja la Beteli amatumikila m’madipatimenti osiyana-siyana, kusamalila nchito yolalikila m’dziko limodzi kapena angapo. Ena amagwila nchito yotembenuza, yosindikiza magazini, yoika zikuto kumabuku, ndipo ena amagwila nchito kosungila mabuku, kopangila ma CD ndi mavidiyo, kapena amasamalila nchito zina zokhudza dela lao.

Komiti ya Nthambi imayang’anila nchito. Bungwe Lolamulila lapeleka udindo wosamalila ofesi ya nthambi iliyonse m’manja mwa Komiti ya Nthambi ya akulu oyenelela atatu kapena oposelapo. Komiti ya Nthambi imadziŵitsa Bungwe Lolamulila za kupita patsogolo kwa nchito ndiponso mavuto amene angabuke m’dela lao. Malipoti amenewa amathandiza Bungwe Lolamulila kuona nkhani zimene angalembe m’zofalitsa zathu ndi mfundo zimene angaphatikize m’nkhani za misonkhano ya mpingo ndi misonkhano ikulu-ikulu. Oimila Bungwe Lolamulila amatumizidwa nthawi ndi nthawi kukacezela nthambi kuti apeleke malangizo ku Komiti ya Nthambi a mmene ingagwilile nchito zake. (Miyambo 11:14) Pamakhala pulogilamu yapadela ndipo, woimila likulu lathu amakamba nkhani yolimbikitsa onse m’dela la nthambi imeneyo.

Amacilikiza mipingo. Abale audindo ku ofesi ya nthambi amavomeleza kuti mipingo yatsopano ikhazikitsidwe. Amayang’anilanso nchito ya apainiya, amishonale, ndi oyang’anila dela amene ali m’dela la nthambi yao. Amakonza misonkhano ikulu-ikulu, amayang’anila nchito yomanga Nyumba za Ufumu zatsopano, ndipo amatsimikiza kuti mabuku amene akufunika atumizidwa kumipingo. Nchito zonse zimene zimacitika ku ofesi ya nthambi zimathandiza kuti nchito yolalikila iziyenda mwadongosolo.—1 Akorinto 14:33, 40.

  • Kodi Makomiti a Nthambi amathandiza Bungwe Lolamulila m’njila ziti?

  • Kodi ni nchito ziti zimene ofesi ya nthambi imasamalila?

DZIŴANI ZAMBILI

Timalandila ndi manja aŵili alendo amene afuna kudzaona maofesi athu a nthambi, kuyambila pa Mande mpaka pa Cisanu. Tikupemphani kuti mukabwele. Pobwela, mukavale mmene mumavalila kumisonkhano. Cikhulupililo canu cidzalimba mukaona malo amenewa ochedwa Beteli.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani