LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w19 November tsa. 31
  • Kodi Mudziŵa?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mudziŵa?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
w19 November tsa. 31
Ku Iguputo wakale, atumiki oyang’anila nyumba anali kuyang’anila anchito amene anali kuseŵenza m’minda

Kodi Mudziŵa?

Kodi mtumiki woyang’anila nyumba anali kugwila nchito yanji m’nthawi yakale?

M’nthawi yakale, mtumiki woyang’anila nyumba anali kuyang’anila zinthu zonse za pa nyumba kapena malo na katundu wa munthu.

Pamene Yosefe mwana wa Yakobo anali kapolo ku Iguputo, anaikidwa kukhala woyang’anila nyumba ya mbuye wake. Ndipo mbuye wakeyo “anasiya zinthu zake zonse m’manja mwa Yosefe.” (Gen. 39:2-6) M’kupita kwa nthawi, Yosefe atakhala wolamulila wamphamvu ku Iguputo, nayenso anaika mtumiki kuti aziyang’anila nyumba yake.—Gen. 44:4.

M’nthawi ya Yesu, anthu amene anali na minda ikulu-ikulu nthawi zambili anali kukhala ku mizinda, kutali na minda yawo. Conco, iwo anali kuika oyang’anila nyumba kuti aziyang’anila anchito amene anali kuseŵenza m’mindayo.

Kodi ni munthu wotani amene anali woyenelela kukhala mtumiki woyang’anila nyumba? Mlembi wina waciroma m’nthawi ya atumwi, dzina lake Columella, anakamba kuti munthu amene anali woyenelela kukhala woyang’anila nyumba anafunika kukhala “munthu woidziŵa bwino nchitoyo.” Anafunikanso kukhala munthu wotha “kuyang’anila ena popanda kucita zinthu molekelela kapena mwankhanza.” Iye anakambanso kuti: “Cofunika kwambili n’cakuti azipewa mzimu wodziona ngati amadziŵa zonse, komanso akhale wokonzeka nthawi zonse kuphunzila zinthu.”

Mawu a Mulungu amaseŵenzetsa citsanzo ca woyang’anila nyumba na nchito imene amagwila pofotokoza nchito zina za mu mpingo wacikhristu. Mwacitsanzo, mtumwi Petulo analimbikitsa Akhristu kuseŵenzetsa maluso amene Mulungu anawapatsa “potumikilana monga oyang’anila abwino amene alandila kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.”—1 Pet. 4:10.

Nayenso Yesu anaseŵenzetsa citsanzo ca woyang’anila nyumba m’fanizo la pa Luka 16:1-8. Komanso, mu ulosi wonena za cizindikilo ca kukhalapo kwake monga Mfumu, Yesu analonjeza otsatila ake kuti adzaika “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” kapena kuti “mtumiki woyang’anila nyumba wokhulupilika.” Nchito yaikulu ya woyang’anila nyumba ameneyu ni kupeleka cakudya cauzimu ca pa nthawi yake, kwa otsatila a Khristu m’nthawi ya mapeto. (Mat. 24:45-47; Luka 12:42) Ndife oyamikila kuti tili pakati pa Akhristu amene amalandila zofalitsa zolimbitsa cikhulupililo, zimene mtumiki woyang’anila nyumba wokhulupilika ameneyu amakonza na kufalitsa padziko lonse.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani