Kubweleza za M’sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa October 29, 2012. Taonetsa deti la mlungu umene tidzaphunzila mfundo iliyonse. Tacita zimenezi kuti mlungu uliwonse tizitha kufufuza mfundozo pokonzekela.
1. Kodi guwa la nsembe limene Ezekieli anaona m’masomphenya likuimila ciani? (Ezek. 43:13-20) [Sept. 10, w07 8/1 tsa. 10 ndime 4]
2. Kodi madzi a mumtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya akuimila ciani? (Ezek. 47:1-5) [Sept. 17, w07 8/1 tsa. 11 ndime 2]
3. Kodi mau akuti “anatsimikiza mumtima mwake,” akusonyeza ciani za mmene Danieli anaphunzitsidwila ali wacinyamata? (Dan. 1:8) [Sept. 24, dp tsa 33-34 ndime 7-9; tsa. 36 ndime 16]
4. Kodi mtengo waukulu womwe Nebukadinezara analota unaimila ciani? (Dan. 4:10, 11, 20-22) [Oct. 1, w07 9/1 tsa. 18 ndime 5]
5. Kodi lemba la Danieli 9:17-19 limatiphunzitsa ciani pa nkhani ya pemphelo? [Oct. 8, w07 9/1 tsa. 20 ndime 5-6]
6. Kodi ndi pangano liti limene ‘anasungila anthu ambili’ mpaka kumapeto kwa mlungu wa 70 wa milungu ya zaka, kapena kuti mu 36 C.E.? (Dan. 9:27) [Oct. 8, w07 9/1 tsa. 20 ndime 4]
7. Kodi zimene mngelo anauza Danieli zakuti “kalonga wa ufumu wa Perisiya” anamutsekeleza zikusonyeza ciani? (Dan. 10:13) [Oct. 15, w11 9/1 tsa. 8 ndime 1-2]
8. Kodi ndi ulosi uti wa m’Baibo wonena za Mesiya umene unakwanilitsika mogwilizana ndi zimene lemba la Danieli 11:20 limanena? [Oct. 15, dp tsa. 232 ndime 5-6]
9. Malinga ndi Hoseya 4:11, kodi pangakhale vuto lanji ngati munthu akumwa moŵa mwaucidakwa? [Oct. 22, w10 1/1 masa. 4-5]
10. Kodi tingaphunzile mfundo yotani pa Hoseya 6:6? [Oct. 22, w07 9/15 tsa. 16 ndime 8; w05 11/15 tsa. 24 ndime 11-12]