Ndandanda ya Mlungu wa October 29
MLUNGU WA OCTOBER 29
Nyimbo 13 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 14 ndime 6-10, ndi bokosi pa tsamba 110 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Hoseya 8–14 (Mph. 10)
Kubweleza za M’sukulu ya Ulaliki (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 108
Mph. 15: “Mmene Mungapindulile ndi Kagulu Kanu ka Ulaliki.” Mafunso ndi mayankho. Pokambilana kabokosi kali patsamba 6, funsani mwacidule wofalitsa amene m’nyumba mwake amacitilamo kukumana kwa ulaliki. Kodi iye amakonza bwanji nyumba yake pasadakhale kaamba ka kukumana kwa ulaliki mlungu ndi mlungu? N’cifukwa ciani iye amayamikila mwai wokhala ndi kukumanako m’nyumba mwake?
Mph. 15: “Njila Zisanu Zopezela Phunzilo la Baibo.” Mafunso ndi mayankho. Mutakambilana ndime 6, pemphani ao amene atsogozapo phunzilo la Baibo lopita patsogolo kuti afotokoze cisangalalo cimene apeza.
Nyimbo 122 ndi Pemphelo