Njila Zisanu Zopezela Phunzilo la Baibo
1. Ngati zimativuta kupeza phunzilo la Baibo m’gawo lathu, kodi tiyenela kucitanji? Ndipo n’cifukwa ninji?
1 Kodi zimakuvutani kupeza munthu wophunzila naye Baibo? Musaleme kufuna-funa. Yehova amadalitsa amene saleka kucita cifunilo cake. (Agal. 6:9) Nazi njila zisanu zimene zingakuthandizeni.
2. Kodi tingagwilitsile nchito bwanji njila yacindunji pofuna kuyambitsa phunzilo?
2 Kupempha Mwacindunji: Anthu ambili amadziŵa kuti timagaŵila magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, koma mwina sadziŵa kuti timapelekanso mwai kwa anthu kuti tiziphunzila nao Baibo. Pamene mulalikila nyumba ndi nyumba, bwanji osayesa kupempha anthu mwacindunji kuti muziphunzila nao Baibo? Mungapemphenso anthu acidwi amene mumaceza nao za Mulungu kuti muyambe kuphunzila nao Baibo. Ngati akana, mungapitilize kumawapatsa zofalitsa zina ndi kulimbikitsa cidwi cao. M’bale wina anali kucezela mwamuna wina ndi mkazi wake kwa zaka zingapo paulendo wake wa magazini. Tsiku lina atawasiila magazini ananyamuka kuti azipita, koma atakumbukila anawafunsa kuti: “Kodi mungakonde kuti tiziphunzila Baibo?” Anadabwa kuona kuti onse avomela. Pano tikamba, onse anabatizika.
3. Kodi tiyenela kuganiza kuti anthu onse acidwi amene amabwela ku misonkhano yathu ali ndi amene amaphunzila nao Baibo? Fotokozani.
3 Obwela ku Misonkhano: Musaganize kuti anthu onse acidwi amene amafika pamisonkhano yathu ali kale ndi owaphunzitsa Baibo. M’bale wina ananena kuti: “Anthu ambili amene ndaphunzila nao Baibo ndinawapeza mwa kufunsa aja amene amabwela ku misonkhano yathu.” Mlongo wina anaganiza zolankhula ndi mzimai wina wamanyazi amene ana ake aakazi anali obatizika mumpingowo. Mzimaiyu anali atasonkhana kwa zaka 15, koma nthawi zonse anali kuloŵa mu Nyumba ya Ufumu misonkhano ikangoyamba ndi kutulukamo ikangotha. Maiyu anavomela kuphunzila naye, ndipo m’kupita kwa nthawi anakhala Mboni. Mlongoyo analemba kuti: “Ndimangodziimba mlandu kuti ndinalola zaka 15 kupita osam’funsapo zophunzila naye!”
4. Kodi tingapeze bwanji phunzilo mwa kufunsa ena?
4 Kufunsa Ena: Mlongo wina amakonda kutsagana ndi ena ku maphunzilo ao a Baibo. Atapempha kwa wotsogoza phunzilo, iye amafunsa wophunzilayo pambuyo pa phunzilo ngati adziŵako aliyense amene angakonde kukhala ndi phunzilo lake-lake. Pogaŵila buku lakuti Baibo Imaphunzitsa kwa munthu amene mumam’cezela, mungam’funse kuti: “Kodi mudziŵako aliyense amene angakonde kukhalako ndi buku ili?” Nthawi zina ofalitsa kapena apainiya sangakwanitse kutsogoza maphunzilo kwa anthu ena amene amakumana nao m’gawo. Conco, dziŵitsani ena kuti ndinu womasuka kutsogoza phunzilo la Baibo.
5. N’cifukwa ciani tiyenela kupempha osakhulupilila, amene amuna ao kapena akazi ao ndi Mboni mumpingo mwathu, ngati angakonde kuphunzila nao?
5 Wapabanja Wosakhulupilila: Kodi mumpingo wanu muli ofalitsa okwatila kapena okwatiwa kwa osakhulupilila? Osakhulupilila ena amakana kukambilana za Baibo ndi anzao a m’cikwati amene ndi Mboni, koma angalole kuphunzila Baibo ndi munthu wina amene si wapabanja pao. Nthawi zonse ndi bwino kufunsila pasadakhale kwa m’bale kapena mlongo njila yabwino yofikila mnzake wa m’cikwati wosakhulupilila.
6. N’cifukwa ciani pemphelo n’lofunika pamene tiyesa-yesa kupeza phunzilo?
6 Pemphelo: Musacepetse mphamvu ya pemphelo. (Yak. 5:16) Yehova amalonjeza kuti adzamva zopempha zathu ngati zigwilizana ndi cifunilo cake. (1 Yoh. 5:14) M’bale wina amene anali wotangwanika kwambili anayamba kupemphela kuti apeze phunzilo la Baibo. Mkazi wake anali kuda nkhawa ngati mwamuna wake angapezedi nthawi yocititsa phunzilo kwa munthu ndi kum’samalila, maka-maka ngati wophunzilayo angakhale ndi mavuto ambili. Conco, mlongoyo anayamba kupemphela kwa Yehova kuti mwamuna wake apeze phunzilo. M’mapemphelo ake anali kuchulamonso nkhawa zakezo. Patangopita milungu iŵili, mapemphelo ao anayankhidwa. Mpainiya wina mumpingo wao anapeza munthu wina amene anali kufuna munthu wophunzila naye, moti anapatsa m’baleyo kuti aziphunzila naye. Poona izi, mkazi wake analemba kuti: “Kwa ao amene aona kuti sangakwanitse kutsogoza phunzilo, ndikuti: Muzichula mwacindunji m’pemphelo lanu cimene mufuna, ndipo musaleke kucipemphelela. Ife tapeza cimwemwe coposa mmene ndinali kuganizila.” Ngati mulimbikila, inunso mungapeze phunzilo la Baibo, ndi kupezanso cimwemwe pothandiza munthu wina kukhala pa ‘mseu wopita ku moyo.’—Mat. 7:13, 14.