Ndandanda ya Mlungu wa November 5
MLUNGU WA NOVEMBER 5
Nyimbo 115 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 14 ndime 11-20 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Yoweli 1–3 (Mph. 10)
Na. 1: Yoweli 2:17-27 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Lemba la Miyambo 22:3 Tingaligwilitsile Nchito Bwanji? (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingaonetse Bwanji Ulemu ku Gulu la Yehova?—rs tsa. 143 ndime 8-12 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 86
Mph. 10: Akazi Amene Amalengeza Uthenga Wabwino ndi Khamu Lalikulu. (Sal. 68:11) Kukambilana kozikidwa pa kabokosi pa tsamba 22, mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2009. Pemphani omvela kuti afotokoze zimene aphunzilapo.
Mph. 10: Zosoŵa za Pampingo.
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini M’mwezi wa November. Nkhani Yokambilana. Fotokozani cifukwa cake magazini awa adzakhala okopa anthu a m’gawo lanu. Citani zimenezi kwa tumphindi 30 mpaka 60. Ndiyeno, pa nkhani zoyambilila zogwilizana ndi mutu wa pacikuto ca Nsanja ya Olonda, pemphani omvela kuti achule funso lodzutsa cidwi limene angafunse poyambitsa makambilano, ndi lemba limene angaŵelenge. Citani cimodzi-modzi ndi Galamukani!, komanso ngati nthawi ilola, citaninso cimodzi-modzi ndi nkhani ina imodzi ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Citani citsanzo ca mmene mungagaŵile magazini iliyonse.
Nyimbo 105 ndi Pemphelo