Zilengezo
◼ Cogaŵila ca October: Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pamaulendo obwelelako, gaŵilani buku lakuti Baibo Imaphunzitsa, kapena malinga ndi mikhalidwe ya munthuyo, mungagaŵile kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. Kenako, yesani kuyambitsa phunzilo la Baibo. November ndi December: Gaŵilani kalikonse ka tumapepala twa uthenga utu: Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa!, Yehova—Kodi Iye Ndani?, Yesu Kristu—Kodi Iye Ndani?, kapena kakuti Kodi Mufuna Kudziŵa Mayankho Azoona pa Mafunso Aya? Ngati munthuyo ali ndi cidwi, gwilitsilani nchito buku lakuti Baibo Imaphunzitsa kumuonetsa mmene timacitila Phunzilo la Baibo. Kapena gwilitsilani nchito kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. January 2013: Gaŵilani kalikonse ka tumabuku twa masamba 32 utu: Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, kapena kakuti Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu. Pamaulendo obwelelako, gaŵilani buku lakuti Baibo Imaphunzitsa. Ngati kungakhale koyenela kwa munthuyo m’gaŵileni kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. Kenako, yesani kuyambitsa phunzilo la Baibo.
◼ Kuyamba ndi kope ino, Utumiki Wathu wa Ufumu uzituluka mu Cinyanja.