LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 10/12
  • Danga la Mafunso

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Danga la Mafunso
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
km 10/12

Danga la Mafunso

Kodi akalinde angathandize bwanji makolo kuti aphunzitse ana ao kusunga khalidwe labwino pamisonkhano?

Mwacibadwa ana amakonda kuseŵela, moti kumakhala kovuta kuti akhazikike kwa nthawi yaitali. Msonkhano ukangotha, amakhala ngati amasuka ndipo amayamba kuthamangitsana mu Nyumba ya Ufumu, kumalo ena osonkhanila, kumalo oikako magalimoto, kapena m’njila zoyendamo. Umanenadi zoona mwambi wakuti: “Mwana womulekelela adzacititsa manyazi mai ake.”—Miy. 29:15.

Comvetsa cisoni n’cakuti acikulile athu ena avulala koopsa cifukwa cogwetsedwa ndi ana. Izi zacititsa mavuto aakulu ndiponso zaonongetsa ndalama zambili za makolo a anawo ndi za mpingo. Pofuna kuteteza ana ndi anthu ena, makolo sayenela kulola ana kuthamanga-thamanga ndi kuseŵela mkati kapena kunja kwa Nyumba ya Ufumu.

Makolo ali ndi udindo wa m’Malemba wophunzitsa ana ao kulemekeza malo athu olambilila. (Mlal. 5:1a) Pamisonkhano ya mpingo ndi misonkhano ikulu-ikulu, akalinde ali ndi nchito yoonetsetsa kuti ‘zinthu zonse zikucitika moyenela ndi mwadongosolo.’ (1 Akor. 14:40; Akol. 2:5) Iwo ayenela kukhala chelu misonkhano isanayambe, ili mkati, ndi pambuyo pake, akumayang’anila mkati mwa Nyumba ya Ufumu ndi panja pomwe. Mwana akayamba kuthamanga-thamanga kapena kuvuta, kalinde akhoza kum’letsa mokoma mtima. Angafotokozele mwanayo cifukwa cake sayenela kucita zimenezo. Ayenela kuuzanso kholo mwaulemu za vutolo ndi kulipempha kuti liyang’anile mwanayo. Kholonso liyenela kucitapo kanthu.

Nthawi zina, makanda ndi ana aang’ono angayambe kulila kapena kusokoneza misonkhano mwa njila zina. Ngati akalinde amafika pamalo osonkhanila pafupi-fupi mphindi 20 misonkhano isanayambe, angasunge mizela ingapo ya mipando yakumbuyo, kuti makolo amene ali ndi ana aang’ono amene angafune akhalepo. Ife ena tiyenela kucilikila makonzedwe amenewa mwa kusakhalapo pa mipando imeneyo.

Ngati mwana asokoneza, kholo lake liyenela kucitapo kanthu. Ngati kholo silicitapo kanthu ndipo mwanayo apitiliza kusokoneza, kalinde apemphe khololo mwaulemu kuti lim’tulutse panja. Tikaitanila kumisonkhano atsopano amene ali ndi ana aang’ono, tiyenela kukhala nao pamodzi kuti tiwathandize kusamalila ana ao akayamba kulila kapena kusokoneza m’njila zina.

Timasangalala kwambili kuona ana a misinkhu yonse pa Nyumba ya Ufumu, ndi kuona khalidwe lao labwino m’nyumba ya Mulungu. (1 Tim. 3:15) Pamene ana alemekeza makonzedwe a kulambila Yehova amam’patsa ulemu, ndipo onse mumpingo amawayamikila kwambili.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani