Ndandanda ya Mlungu wa December 10
MLUNGU WA DECEMBER 10
Nyimbo 32 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 16 ndime 1-7, ndi bokosi patsamba 128 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Zefaniya 1–Hagai 2 (Mph. 10)
Na. 1: Hagai 1:1-13 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Anthu Anayamba Bwanji Kutsatila Nzelu za Anthu?—rs tsa.137 ndime 1-3 (Mph. 5)
Na. 3: Kukhala ndi Maganizo a Kristu Kumatithandiza Kudziŵa Kwambili Yehova—Mat. 11:27 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 107
Mph. 15: Sukulu ya Ulaliki ya 2013. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anila sukulu. Kambitsilanani mfundo zimene zingapindulitse mpingo wanu mwa kugwilitsila nchito malangizo a Sukulu ya Ulaliki ya 2013. Limbikitsani onse kuti aziyesetsa kukwanilitsa mbali zao, kutengako mbali pa mfundo zazikulu, ndi kugwilitsila nchito malingalilo opelekedwa mlungu uliwonse a mu buku la Sukulu ya Utumiki.
Mph. 15: “Khalani Mwamtendele ndi Anthu Onse.” Mafunso ndi mayankho. Khalani ndi zitsanzo ziŵili zacidule. Coyamba cionetse wofalitsa ayankha mwaukali mwininyumba amene alankhula naye mokwiya, ndipo caciŵili wofalitsa ayankha mofatsa.
Nyimbo 39 ndi pemphelo