LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 12/12 tsa. 2
  • “Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu . . .”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu . . .”
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
km 12/12 tsa. 2

“Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu . . .”

Mwezi uliwonse pa Msonkhano wa Nchito, timakhala ndi nkhani yofotokoza mmene tingagaŵilile magazini. Colinga cake sikuona zimene zili m’magazini. Koma kukambilana njila zogaŵila magaziniwo. Ndiye cifukwa cake, malinga ndi malangizo, mau oyamba a m’bale wokamba nkhaniyi amakhala acidule kwambili kuti adzutse cidwi ca abale pa magaziniwo. Ndiyeno, amapempha ofalitsa kukambapo pa nkhani imodzi (kapena zingapo zimene zili pansi pa mutu umodzi waukulu) asanapite pa ina, kuti onse azitsatila ndi kuona zimene angakambe pogaŵila magaziniwo. Iye sapempha omvela kuti anene ulaliki wonse umene akonzekela, koma amapempha ofalitsa kunena mafunso amene angadzutse cidwi m’delalo, ndiyeno amawapempha kunena malemba amene angakaŵelenge. Pomaliza, amaitanitsa zitsanzo zoonetsa mogaŵilila magazini iliyonse. Ndi bwino kuŵelengelatu magazini kunyumba kuti tiziyankhapo. Ndipo ngati tonse tikonzekela bwino, nkhani imeneyi idzatithandiza kuti tinolane.—Miy. 27:17.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani