Ndandanda ya Mlungu wa December 24
MLUNGU WA DECEMBER 24
Nyimbo 5 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 16 ndime 13-18 (Mph.30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Zekariya 9–14 (Mph.10)
Na. 1: Zekariya 11:1-13 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Mulungu Amakhala Wofunitsitsa Kumva Mapemphelo a Anthu Otani?—rs tsa. 339 ndime 3-tsa. 340 ndime 6 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingagwilitse Nchito Mfundo ya pa Miyambo 15:1 pa Nthawi Iti? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 75
Mph. 10: Tiyeni Tigwilitsile Nchito Bwino Webu Saiti Yathu. Nkhani yocokela mu mphatika pa masamba 3-6. Dziŵitsani abale za Webu Saiti yathu ya jw.org. Ngati abale sadziŵa za makompyuta, limbikitsani mabanja kukhala ndi laibulale yaing’ono ya mabuku athu kunyumba kwao. Muwalimbikitse kucita zimenezi mukatsiliza kufotokoza mwacidule mfundo za m’mphatika.
Mph. 10: Mabanja Acikristu, Khalani Maso. Nkhani ndi mbali yofunsa mafunso, yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya May 15, 2011, masamba 7 mpaka 11. Pambuyo pofotokoza mwacidule nkhaniyo kwa mphindi 5, kambilanani ndi tate, mai ndi wacinyamata. Apempheni kufotokoza zimene amacita kuti alimbitse uzimu wa banja lao.
Mph. 10: Kodi Mukupindula ndi Kulambila kwa Pabanja? Nkhani ndi kukambilana ndi omvela, yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya August 15, 2011 tsamba 6. Funsani omvela kuti afotokoze njila zimene aona kuti n’zothandiza pa kulambila kwao kwa pabanja ndi cifukwa cake njilazo n’zothandiza.
Nyimbo 101 ndi Pemphelo