Ndandanda ya Mlungu wa December 17
MLUNGU WA DECEMBER 17
Nyimbo 97 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 16 ndime 8-12, ndi bokosi patsamba 132 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Zekariya 1-8 (Mph. 10)
Na. 1: Zekariya 8:1-13 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Yehova Ndi Ambuye Wamkulu Koposa?—Sal. 73:28 (Mph. 5)
Na. 3: N’cifukwa Ciani Anthu Oganiza Bwino Amaphunzila Zimene Yesu Kristu Ankaphunzitsa, M’malo Mwa Nzelu za Anthu?—rs tsa. 138 ndime 1–tsa. 139 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 65
Mph. 5: “Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu . . .” Kukambilana.
Mph. 10: Uthenga Umene Tiyenela Kulengeza—‘Opani Mulungu Woona, Sungani Malamulo Ake.’ Nkhani yogwila mtima yocokela m’buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 272, mpaka pa kamutu patsamba 275.
Mph. 15: Kodi Mwayesapo Kuzigwilitsila Nchito? Kukambilana. Kambani nkhani yacidule yofotokoza mfundo zazikulu za nkhani izi za mu Utumiki Wathu wa Ufumu waposacedwa: “Muzilalikila Molimba Mtima Kumalo a Nchito ndi Amalonda” (km 3/12) “Thandizani Anthu Kuti Azimvela Mulungu” (km 8/12), ndi “Kodi Mukhoza Kumacitako Ulaliki wa M’madzulo?” (km 10/12). Kenako pemphani omvela kuti akambe mapindu amene apeza mwa kugwilitsila nchito malingalilo a mu nkhani zimenezi.
Nyimbo 117 ndi Pemphelo