Zilengezo
◼ January ndi February: Gaŵilani kalikonse ka tumabuku ta masamba 32 utu: Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, kapena kakuti Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu. Pamaulendo obwelelako, gaŵilani buku lakuti Baibo Imaphunzitsa. Ngati kungakhale koyenela kwa munthuyo, m’gaŵileni kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. Kenako, yambitsani phunzilo la Baibo. March ndi April: Gaŵilani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pamaulendo obwelelako, gaŵilani buku lakuti Baibo Imaphunzitsa. Ngati kungakhale koyenela kwa munthuyo, m’gaŵileni kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. Kenako, yambitsani phunzilo la Baibo.
◼ Mutu wa nkhani ya onse imene woyang’anila dela azikamba kuyambila mwezi wa March 2013, idzakhala ndi mutu wakuti: “Uthenga Wabwino . . . Kudziko Lililonse, Fuko Lililonse, ndi Cinenelo Ciliconse.”
◼ Ofalitsa amene afuna kucita upainiya wothandiza mu mwezi wa March 2013, adzakhala ndi mwai wosankha mlingo wa maola 30 kapena 50 m’mwezi umenewo. Ndiponso ngati woyang’anila dela acezela mpingo mu March, onse amene acita upainiya wothandiza adzapezekapo pa msonkhano wonse wa woyang’anila dela ndi apainiya a nthawi zonse.
◼ Mu miyezi 6 yapita, mipingo 8 inapatulila Nyumba zao za Ufumu zatsopano kwa Yehova. Mipingo imeneyi ndi Mpula, Mitumba, Chenda, Lweenge, Lusaka Matero North West, Kafumukache, ndi Chimpasha.