Ndandanda ya Mlungu wa February 4
MLUNGU WA FEBRUARY 4
Nyimbo 70 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 18 ndime 12-18 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Mateyu 22-25 (Mph. 10)
Na. 1: Mateyu 23:25-39 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: N’cifukwa Ciani Akristu Ayenela Kucita Cidwi ndi Maulosi a m’Baibo?—rs tsa. 390 ndime 3-7 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi ndi Anthu Ati Ochulidwa m’Baibo Omwe Anatsatila Malangizo a pa Miyambo 3:5? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 37
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu February. Kukambilana. Fotokozani cifukwa cake magazini awa adzakhala okopa anthu a m’gawo lanu. Citani zimenezi kwa tumphindi 30 mpaka 60. Ndiyeno, pa nkhani zoyambilila zogwilizana ndi mutu wa pacikuto ca Nsanja ya Olonda, pemphani omvela kuti achule funso lodzutsa cidwi limene angafunse poyambitsa makambilano, ndi lemba limene angaŵelenge. Citani cimodzi-modzi ndi Galamukani! komanso ngati nthawi ilola, citaninso cimodzi-modzi ndi nkhani ina imodzi ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Citani citsanzo ca mmene mungagaŵilile magazini iliyonse.
Mph. 10: Ngati Wina Anena Kuti, ‘Sindimakhululupila Mulungu.’ Nkhani yokambilana yocokela m’buku la Kukambitsilana, tsamba 311, ndime 5 mpaka tsamba 312, ndime 2. Khalani ndi citsanzo cacidule cimodzi.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Nyimbo 95 ndi Pemphelo