LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 1/13 tsa. 3
  • Cikondi ca Kristu Cimatilimbikitsa Kukonda Ena

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cikondi ca Kristu Cimatilimbikitsa Kukonda Ena
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 1/13 tsa. 3

Cikondi ca Kristu Cimatilimbikitsa Kukonda Ena

1. Kodi citsanzo ca Yesu cimatilimbikitsa kucita ciani?

1 Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili pa nkhani ya cikondi. Iye anapeleka citsanzo cabwino kwambili cimeneci, kuti otsatila ake azicita zinthu motsatila cikondi cimeneco.—Aroma 8:35.

2, 3. Kodi Mboni za Yehova zimadziŵika ndi mbili yotani kulikonse?

2 Mboni za Yehova zimadziŵika cifukwa cosonyezana cikondi ngati ca Kristu. Ganizilani ao amene anadzipeleka kuthandiza anzao pamene mphepo yamkuntho inasakaza madela ambili ku United States mu 2005. Anthu oposa 20,000 anadzipeleka kuthandiza abale ao ovutika.

3 Kudela lina, madzi a m’nyanja anasefukila kufika pamtunda wamakilomita 80 kucokela kunyanja, ndipo anali akuya mamita 10. Madziwo ataphwila, nyumba imodzi mwa zitatu zilizonse za anthu komanso nyumba zina, zinali zitaonongekelatu. Abale ndi alongo aluso ocokela m’maiko osiyana-siyana anafika kudelali ndi zida ndiponso katundu womangila, ndipo anali okonzeka kugwila nchito iliyonse imene ingafunike. Cimeneco n’citsanzo cabwino coonetsa maganizo a Kristu.

4, 5. N’ciani cidzatilimbikitsa kuthandiza ena?

4 Ambili a ife sitinakumanepo ndi masoka akulu-akulu acilengedwe. Koma tonse timakumana ndi vuto la matenda, mwina ifeyo kudwala kapena wacibale. Cifukwa ­cokonda anthu, Yesu anacitila cifundo odwala amene makamu a anthu anamubweletsela. Ndipo “onse amene sanali kumva bwino m’thupi anawacilitsa.”—Mat. 8:16; 14:14.

5 Ifenso tiyenela kukhala ndi mtima wacifundo ngati Yesu. Taganizilani za Charlene wa zaka 44, amene anali ndi kansa ndipo anauzidwa kuti adzamwalila pakapita masiku 10. Alongo aŵili, Sharon ndi Nicolette, anadzipeleka kumusamalila masiku onse omaliza a moyo wake. Mlongoyu anakhalabe ndi moyo mpaka milungu 6. Sharon anati: “Zimakhala zovuta ngati wadziŵa kuti munthuyo sadzacila. Koma Yehova anatipatsa mphamvu. Zimene zinacitikazi zinatithandiza kukonda kwambili Mulungu ndi kukondana.” Mwamuna wa Charlene anati: “Sindidzaiŵala kukoma mtima kwa alongo aŵili okondedwa amenewa ndi ­thandizo limene anapeleka. Thandizo lao locokela pansi pa mtima ndi cilimbikitso cao, zinathandiza kuti mkazi wanga apilile ciyeso cake comaliza. Ndipo ndidzapitilizabe kuwayamikila. Mtima wao wodzimana unalimbitsa cikhulupililo canga mwa Yehova ndi cikondi canga pa gulu lonse la abale.”

6. N’ciani cimene tiyenela kukumbukila kucita?

6 Kodi mungacititse kuti cikondi canu caubale cizionekela mumpingo mwanu? Tizisonyeza cikondi ca Kristu kwa abale athu onse, ngati mmene Kristu anacitila “mpaka pa mapeto.” Cikondi coteleci cimasonyeza kuti ndife otsatila eni-eni a Yesu.—Yoh. 13:1, 34, 35.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani