Ndandanda ya Mlungu wa February 11
MLUNGU WA FEBRUARY 11
Nyimbo 106 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 18 ndime 18-24 (Mph.30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Mateyu 26-28 (Mph.10)
Na. 1: Mat. 27:24-44 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Kuleza Mtima Kwa Mulungu Kukuthandiza Bwanji Kuti Anthu Adzapulumuke?—2 Pet. 3:9, 15 (Mph. 5)
Na. 3: Ngati wina wanena kuti, ‘Mumakonda Kunena Kwambili za Maulosi’—rs tsa 390 ndime8–tsa. 391 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 31
Mph. 10: Tiphunzilapo Ciani? Ŵelengani Mateyu 6:19-21; Luka 16:13 ndipo kambilanani mmene malembawa angatithandizile mu utumiki.
Mph. 20: “Kodi Mudzacitako Upainiya Wothandiza?” Mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi woyang’anila utumiki. Pambuyo pokambilana ndime 2, mwacidule funsani ofalitsa aŵili amene afuna kucitako upainiya wothandiza m’mwezi wa March, wina akhale wolembedwa nchito ndipo winayo akhale amene sacita zambili mu utumiki kaamba ka vuto la thanzi. Afunseni makonzedwe amene apanga kuti adzaciteko upainiya. Pambuyo pokambilana ndime 3, khalani ndi citsanzo coonetsa Akristu aŵili okwatilana kapena banja limene lili ndi ana, likucita Kulambila kwa Pabanja kuti lipange makonzedwe a mmene angafutukulile utumiki wao.
Nyimbo 122 ndi Pemphelo