Ndandanda ya Mlungu wa February 18
MLUNGU WA FEBRUARY 18
Nyimbo 52 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 19 ndime 1-5 masamba 149-150 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Maliko 1–4 (Mph.10)
Na. 1: Maliko 2:18–3:6 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi ciphunzitso ca Purigatoriyo Cinacokela Kuti?—rs tsa 343 ndime 1-tsa 344 ndime 3 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Malangizo Amene Paulo Ananena pa 1 Akorinto 7:29-31 Amatanthauza Ciani? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo92
Mph. 15: Lalikilani M’nthawi Yovuta. (2Tim. 4:2) Nkhani yokambilana yocokela mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2012 tsamba8-9, ndi Nsanja ya Olonda ya January 15, 2012 tsamba14. Pemphani omvela kuti afotokoze zimene anaphunzila.
Mph. 15: “Nchito yapadela yoitanila Anthu ku Cikumbutso Idzayamba pa March 1.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Gaŵilani onse ali m’gulu kapepala koitanila anthu ndipo kambilanani zimene zili pa kapepalako. Pokambilana ndime 2, itanani woyang’anila utumiki kuti afotokoze makonzedwe amene apangidwa kuti anthu ambili aitanidwe m’gao lanu. Pokambilana ndime 3, citani citsanzo ca mmene tingakagaŵile.
Nyimbo8 ndi Pemphelo