Ndandanda ya Mlungu wa February 25
MLUNGU WA FEBRUARY 25
Nyimbo 120 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 19 ndime 6-11 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Maliko 5–8 (Mph.10)
Kubweleza za M’sukulu ya Ulaliki (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 135
Mph. 5: “Musaleke.” Nkhani yokambilana.
Mph. 10: Uthenga Umene Tiyenela Kulengeza ‘Kucitila Umboni za Yesu.’ Nkhaniyi ikambidwe mwaumoyo, ndipo icokela m’buku la Pindulani, pa tsamba 275 mpaka kumapeto kwa tsamba 278.
Mph. 15: Yehova Amatipatsa Mphamvu kuti Tilalikile. (Afil. 4:13) Funsani ofalitsa aŵili kapena atatu amene amalalikila mwacangu ngakhale kuti amavutika ndi matenda. Kodi amakumana ndi mavuto ati? N’ciani cimawathandiza kuti asamakhale okhumudwa kwa nthawi yaitali? Kodi mpingo waŵathandiza bwanji? Kodi apindula bwanji cifukwa cotenga mbali nthawi zonse mu ulaliki?
Nyimbo 42 ndi Pemphelo