Ndandanda ya Mlungu wa April 1
MLUNGU WA APRIL 1
Nyimbo 38 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 21 ndime 1-7 ndi bokosi pa tsa. 166 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Luka 7–9 (Mph. 10)
Na. 1: Luka 7: 18-35 (Mph.4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Ndi Mtundu Watsopano uti Umene Unabadwa pa Pentekosite, Ndipo Colinga Cake Cinali Ciani?—Agal. 6:16;1 Pet. 2:9 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mkazi Amene Kaini Anakwatila Anacokela Kuti?—w10/1 tsa 25 mfundo imeneyi yafotokozedwa bwino mu rs tsa 235 ndime 2-4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 113
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu April. Kukambilana. Fotokozani cifukwa cake magazini awa adzakhala okopa anthu a m’gawo lanu. Citani zimenezi kwa tumphindi 30 mpaka 60. Ndiyeno, pa nkhani zoyambilila zogwilizana ndi mutu wa pacikuto ca Nsanja ya Olonda, pemphani omvela kuti achule funso lodzutsa cidwi limene angafunse poyambitsa makambilano, ndi lemba limene angaŵelenge. Citani cimodzi-modzi ndi Galamukani! komanso ngati nthawi ilola, citaninso cimodzi-modzi ndi nkhani ina imodzi ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Citani citsanzo ca mmene mungagaŵilile magazini iliyonse.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Muligwilitsile nchito bwino Yearbook ya 2013. Kukambilana. Kambilanani “Kalata yocokela ku Bungwe Lolamulila.” Mukonze zakuti ena akakonzekele pasadakhale zoti akakambepo pa zitsanzo zolimbikitsa zocokela mu Yearbook. Pemphani omvela kuti afotokoze mbali zocititsa cidwi za lipoti yapadziko lonse. Mukafika kumapeto limbikitsani onse kuti amalize kuŵelenga Yearbook.
Nyimbo 75 ndi Pemphelo