Zilengezo
◼ Cogaŵila ca mu May ndi June: Gaŵilani kalikonse ka tumapepala twa uthenga utu: Kodi Ndani Kweni-kweni Akulamulila Dziko?, kapena kakuti Kodi Mufuna Kudziŵa Mayankho Azoona pa Mafunso Aya? Ngati munthuyo ali ndi cidwi, gwilitsilani nchito buku lakuti Baibo Imaphunzitsa kumuonetsa mmene timacitila Phunzilo la Baibo. Kapena gwilitsilani nchito kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. July ndi August: Mungagwilitsile nchito kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu! kapena kalikonse ka masamba 32 mwa tumabuku utu: Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!, Mvetselani kwa Mulungu ndi kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya.