Ndandanda ya Mlungu wa June 3
MLUNGU WA JUNE 3
Nyimbo 68 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 24 ndime 1-9 ndi bokosi patsamba 193 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Yohane 17–21 (Mph. 10)
Na. 1: Yohane 21:15-25 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi N’cifukwa Ciani Sitiyenela ‘Kutsatila Khamu’?—Eks. 23:2; Miy. 1:10 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ndani Amenenso Akupindula Ndi Nsembe ya Yesu?—rs tsa. 125 ndime 1-3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 16
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu June. Kukambilana. Fotokozani cifukwa cake magazini awa adzakhala okopa anthu a m’gawo lanu. Citani zimenezi kwa tumphindi 30 mpaka 60. Ndiyeno, pa nkhani zoyambilila zogwilizana ndi mutu wa pacikuto ca Nsanja ya Olonda, pemphani omvela kuti achule funso lodzutsa cidwi limene angafunse poyambitsa makambilano, ndi lemba limene angaŵelenge. Citani cimodzi-modzi ndi Galamukani! komanso ngati nthawi ilola, citaninso cimodzi-modzi ndi nkhani ina imodzi ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Citani citsanzo ca mmene mungagaŵilile magazini iliyonse.
Mph. 10: Cifukwa Cimene Timapelekela Lipoti la Utumiki Wathu wa Kumunda. Nkhani yokambidwa ndi kalembela, yocokela m’buku la Gulu, patsamba 88, ndime 1 mpaka tsamba 90, ndime 1.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Nyimbo 107 ndi Pemphelo