Kodi Ndi ‘Ozikika Mozama’ ndi ‘Okhazikika m’Cikhulupililo’?
N’cifukwa ciani zomela zambili zili ndi mizu? Mizu imathandiza comela kuti cikhazikike zolimba m’nthaka. Imatenga madzi ndi cakudya cina m’nthaka. Mizu ina imatulutsa mphukila imene imakula kukhala zomela zatsopano. Kodi tingayelekeze anthu amene timaphunzila nao Baibo ndi zomela zimene zikukula? Inde. Timagwila nchito yobzala mbeu za Ufumu ndi kuthilila pamodzi ndi Mulungu monga anchito anzake. Yehova amacita mbali yake mwa ‘kuzikulitsa.’—1 Akor. 3:6.
Monga mmene comela cimene cikukula cimafunikila mizu yabwino, atsopano naonso afunika kukhala ndi maziko abwino m’coonadi. Amafunika mizu ndipo afunikila kukhala ‘ozikika mozama’ mwa Kristu ndi ‘okhazikika m’cikhulupililo’ kuti apambane mayeselo amene angakumane nao. (Akol. 2:6, 7; 2 Tim. 3:12; 1 Pet. 5:8, 9) Kuonjezela pamenepa, kuti azitha kuphunzitsa ena mogwila mtima, ayenela kukhala “odziŵa coonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Buku lakuti Zimene Baibo Limaphunzitsa limathandiza kwambili ophunzila kudziŵa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo, ndipo buku lakuti, Cikondi ca Mulungu limawathandiza kuganizila malamulo a Mulungu ndi mfundo zake. Bukuli lakonzedwa n’colinga cotithandiza kukambitsilana momasuka ndi ophunzila amene akupita patsogolo nkhani monga kavalidwe ndi maonekedwe, ukhondo, zosangulutsa, ndi kusankha bwino anthu oceza nao.—lv mas. 50-73.
Ophunzila Baibo ena amapita patsogolo mwamsanga ndipo m’nthawi yocepa amabatizika akangotsiliza buku la Zimene Baibo Limaphunzitsa. Kodi zikakhala conco, timasiya kuthandiza ‘mbeu’ zimene zikukulazi? Iyai. Pitilizani kuphunzila ndi wophunzila Baibo wopita patsogoloyo mpaka akamalize mabuku aŵili. Mabuku amenewa ndio Zimene Baibo Limaphunzitsa ndi ‘Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu.’ Pambuyo pa ubatizo wao, tingapitilizebe kucita lipoti nthaŵi imene tiphunzila nao, maulendo obwelelako, ndi phunzilo kwa nthaŵi yocepa imene tingatenge kuti titsilize mitu yotsala m’buku laciŵili. Ngati wofalitsa wina apita nafe ku phunzilo limeneli ndipo alankhulapo, iyenso angacitile lipoti nthaŵi.—Onani bokosi la mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November ndi wa March 2009, tsamba 2.
Mizu ya comela sionekela poyela, koma ndi yofunika kwambili ku comelaco. Imacipangitsa kukhala cokhazikika ndipo imapeleka cakudya. Mofananamo, citsanzo ca Kristu ndi ciphunzitso cake zimasonkhezela anthu acidwi, coyamba mosaonekela, kenako zimakhazikika m’maganizo ndi m’mitima yao. Pang’ono-pang’ono zimawakhutilitsa ndi kuwalimbitsa. Pamene alola ziphunzitso zimenezi kulamulila maganizo ao, zocita ndi zosankha zao, amalimbikitsidwa kudzipeleka kwa Yehova ndi kupitiliza m’njila ya coonadi. Zimenezi zimatisangalatsa kwambili.—1 Pet. 2:21; 3 Yoh. 4.