Kodi Mwana Wanu Amanyamula Khadi Lake?
Mungaitanitse khadi la Mwana (ic) kupyolela kumpingo. Khadi limeneli limadziŵikitsa ana a Mboni osabatizika. Khadili lili ndi adiresi ndi nambala ya foni ya makolo. Imafotokoza bwino cithandizo ca mankhwala cosagwilitsila nchito magazi cimene mungasankhile mwana wanu. Mwana wanu ayenela kunyamula khadi limeneli nthawi zonse.
Kuonjezela pa Khadi la Mwana, acicepele acikristu ayenela kufotokoza momveka bwino ndi molimba mtima zimene io amakhulupilila pankhani yoika magazi. (Mac. 15:28, 29) Makolo angaziyeselela ndi ana ao kuti awathandize kudziŵa bwino kufotokoza zimene amakhulupilila. Kodi ndinu wotsimikiza kuti mwana wanu aliyense wobatizika ali ndi DPA ndi kuti mwana aliyense wosabatizika amanyamula Khadi la Mwana?
[Bokosi papeji 6]
KHADI LA MWANA
(Dzina la mwana)
Makolo:
(Adiresi)
(Foni ya kunyumba)
(Foni ya m’manja)
ONANI MKATI MAU OFUNIKA OKHUDZA ZACIPATALA
Monga makolo timasamala kwambili za moyo wa mwana wathu, ________________
Ndife Mboni za Yehova ndipo tili ndi cikhulupililo colimba pa mfundo za m’Baibo zimene timakhulupilila. Pacifukwa cimeneci, sitilola kuikidwa magazi. (Mac. 15:29) Anthu ambili amadziŵa kuti kuikidwa magazi, ngakhale anthu a magulu a magazi ofanana, kuli ndi ngozi yopeleka matenda otupa ciwindi, HIV, ndi matenda ena. Podziŵa zimenezo, ife tasankha kupewa ngozi zotelozo. Komabe, timalandila mankhwala oculukitsa magazi ochedwa nonblood expanders, mankhwala oletsa kukha magazi amenenso amathandiza kupanga maselo ofiila a magazi, ndi mankhwala ena osasakanizako magazi. Ngati mwana wathu apezeka m’ngozi kapena adwala mwakaya-kaya, conde tidziŵitseni mwamsanga. Timadziŵa madokotala amene amalemekeza cikhulupililo cathu ndipo ndi okonzeka kutithandiza pogwilitsa nchito mankhwala ena amakono osaphatikizapo magazi.
(Siginecha)
(Deti)
(Siginecha)
(Deti)