Ndandanda ya Mlungu wa March 10
MLUNGU WA MARCH 10
Nyimbo 1 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 5 ndime 13-18 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Genesis 40-42 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 41:1-16 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Mmene Otsala a Akufa Adzabwelelenso Kumoyo Padziko Lapansi—rs tsa. 112 ndime 1-4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tiyenela Kucita Zinthu Motani Ndi Munthu Wocotsedwa?—lv tsa. 207-209 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 88
Mph. 15: Kulambila kwa Pabanja Kosangalatsa. Funsani banja kuti lifotokoze za ndandanda yao ya kulambila kwa pabanja. Kodi pandandanda yao pamakhala zotani? Nanga amasankha bwanji zofunika kukambitsilana? Ndi zinthu zotani zopezeka pa jw.org zimene agwilitsilapo nchito? Nanga ndandanda yao yawathandiza bwanji mu utumiki? Amacita ciani kuti zinthu zina zisasokoneze ndandanda yao? Nanga apindula bwanji ndi ndandanda yakulambila kwa pabanja?
Mph. 15: “Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Mmene Tingayankhile Anthu Amene Safuna Kuti Tikambitsilane Nao.” Nkhani yokambitsilana. Kambitsilanani njila ziŵili kapena zitatu zimene anthu amene asafuna kukambilana nafe angagwilitsile nchito. Ndipo pemphani ofalitsa kuti afotokoze mmene angayankhile. Kumbutsani ofalitsa kuti mlungu wa April 7 adzakhala ndi mwai wofotokoza zocitika za mu utumiki.
Nyimbo 97 ndi Pemphelo