Zilengezo
Zogaŵila mu: March ndi April: Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani! May ndi June: Zimene Baibo Imaphunzitsa kapena kamodzi mwa tumapepala twauthenga totsatila: Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?, Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?, Kodi Cofunika N’ciani Kuti Banja Likhale Lamtendele?, Kodi Ndani Maka-maka Amene Akulamulila Dzikoli?, Kodi Mavuto Adzathadi?, ndi kakuti Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?
Cikumbutso cidzakhalako pa Mande, April 14, 2014. Ngati mpingo wanu umasonkhana pa Mande, mungasankhe tsiku lina lililonse mlungu umenewo pamene ena sagwilitsila nchito Nyumba ya Ufumu. Ngati simudzakhala ndi Msonkhano wa Nchito mlungu umenewo, mgwilizanitsi wa bungwe la akulu ayenela kusintha ndandanda kotelo kuti nkhani zofunika kwambili zidzakambidwe ku mpingo mwezi umenewo.
Nkhani ya onse imene woyang’anila dela azikamba pa ulendo wake waciwili mu caka ca utumiki ca 2014 ili ndi mutu wakuti, “Posacedwapa Tidzapulumutsidwa ku Masutso a Dziko”