Ndandanda ya Mlungu wa April 7
MLUNGU WA APRIL 7
Nyimbo 15 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 6 ¶19-24, ndi bokosi patsamba 78 (30 min.)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Ekisodo 7–10 (Mph. 10)
Na. 1: Ekisodo 9:20 mpaka 35 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Mmene Kubwela kwa Yesu Kudzakhalile Ndiponso Mmene Diso Lililonse Lidzamuonele—rs tsa 163 ndime 3 mpaka tsa. 164 ndime 4 (Mph. 5)
Na. 3: Muzikhala Wokhulupilika Ndiponso Wokonzeka Kuthandiza Abale Anu—lv tsa. 33 mpaka 34 ndime 16-18. (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 124
Mph. 10: Kugaŵila Magazini m’Mwezi wa April. Nkhani yokambitsilana. Yambani nkhaniyi mwa kucita citsanzo ca zimene tingacite pogaŵila magazini. Gwilitsilani nchito maulaliki acitsanzo amene ali patsamba lino. Ndiyeno kambitsilanani maulaliki onse acitsanzo. Mwacidule malizani mwa kulimbikitsa onse kuti aziŵelenga magazini ndi kuwagaŵila kwa ena mokondwela.
Mph. 10: Musaiŵale Kuceleza Alendo. (Aheb. 13:1, 2) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Fotokozani makonzedwe amene mpingo wapanga kaamba ka Cikumbutso. Chulani zimene onse angacite kuti akaceleze alendo ndi ofalitsa ozilala amene adzapezeka pa Cikumbutso. Citani citsanzo cacidule ca mbali ziŵili. Citsanzo coyamba, cionetse wofalitsa akulandila munthu amene analandila ciitano cobwela ku Cikumbutso, wofalitsa akucita zimenezi misonkhano isanayambe. Caciŵili, pambuyo pa misonkhano wofalitsa akupanga makonzedwe okacezela mlendo amene anaonetsa cidwi.
Mph. 10: Kodi Tinacita Zotani? Nkhani yokambitsilana. Pemphani omvela kuti afotokoze mapindu amene apeza pogwilitsila nchito mfundo za m’nkhani yakuti, “Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Mmene Tingayankhile Anthu Amene Safuna Kuti Tikambitsilane Nao.” Pemphani omvela kuti asimbe zocitika zabwino za mu ulaliki.
Nyimbo 20 ndi Pemphelo