Ndandanda ya Mlungu wa August 4
MLUNGU WA AUGUST 4
Nyimbo 51 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 12 ndime 1 mpaka 7 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Numeri 4-6 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 4:17-33 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Baibulo Limati Ena Sadzapulumutsidwa Konse—rs tsa. 95 ndime 3-tsa 96 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Yehova Amaweluza Anthu Amene Amanamizila Ena Milandu—lv tsa. 137 ndime 11-12 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 85
Mph. 10: Kugaŵila Magazini mu August. Kukambilana. Citani citsanzo coonetsa mmene tingagaŵile magazini pa kutha kwa mlungu pamene tikugwila nchito yapadela, pogwilitsila nchito maulaliki acitsanzo amene ali pa tsamba lino. Ndiyeno pemphani omvela kuti ayankhe mafunso awa: N’cifukwa ciani tiyenela kugaŵila magazini m’mwezi wa August pa mapeto a mlungu ngati m’pofunika kutelo? Ndi pa zocitika zinanso ziti pamene zimenezi zingatheke?
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Kodi Tinacita Zotani? Kukambilana. Pemphani ofalitsa kuti anene mmene apindulila pogwilitsila nchito nkhani yakuti “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano ndi Colinga Cakuti Ticite Ulaliki Wamwai.” Pemphani omvela kuti afotokoze zokumana nazo zabwino.
Nyimbo 75 ndi Pemphelo