Ndandanda ya Mlungu wa September 22
MLUNGU WA SEPTEMBER 22
Nyimbo 9 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 14 ndime 1 mpaka 7 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Numeri 30-32 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 32:16-30 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi N’cifukwa Ciani Mulungu Sanaononge Satana Mwamsanga Atangopanduka—rs tsa. 354 ndime–2 tsa. 355 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: N’cifukwa ciani Adamu ndi Hava Sanamvele Yehova—bh tsa. 61 ndime 9-11 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 93
Mph. 15: Umoyo wa Umishonale ndi Wopindulitsa. (Miy. 10:22) Nkhani yokambilana kucokela m’Buku lapacaka la 2014, pa tsamba 123, ndime 2, mpaka tsamba 127, ndime 4, ndiponso tsamba 169. Pemphani omvela kuti afotokoze zimene aphunzilapo.
Mph. 15: “Gwilitsani Nchito Webusaiti ya jw.org mu Ulaliki.” Nkhani yokambilana. Citani citsanzo ca ulaliki umene uli m’ndime 2. Pambuyo pake funsani gulu mafunso awa: Kodi kukopela kavidiyo pa foni kapena pa tabuleti yanu kuli ndi phindu lanji? N’cifukwa ciani simuyenela kukamba mau ambili kwa mwininyumba musanamuonetse kavidiyo? Nanga n’cifukwa ciani ndi bwino kuyamba kuonetsa mwininyumba kavidiyo kameneka ngakhale tisanam’pemphe cilolezo? Ndi zocitika za mu utumiki zotani zimene munakhala nazo pogwilitsila nchito kavidiyo kameneka? Malizani mwa kulimbikitsa ofalitsa kuti azidziŵa bwino zinthu zosiyanasiyana zimene zimapezeka pa Webusaiti yathu ya jw. org ndi kuigwilitsila nchito mu ulaliki wao. Ngati kwanuko kulibe amene ali ndi foni kapena tabuleti yokhala ndi intaneti, gwilitsilani nchito Utumiki Wathu wa Ufumu wa December 2012, tsamba 3.
Nyimbo 84 ndi Pemphelo